Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

TURKMENISTAN

Mfundo Zachidule Zokhudza a Mboni ku Turkmenistan

Mfundo Zachidule Zokhudza a Mboni ku Turkmenistan

A Mboni za Yehova akhala akupezeka ku Turkmenistan kuyambira chakumapeto kwa zaka za m’ma 1980. Dzikoli litangolandira ufulu wodzilamulira kuchokera ku ulamuliro wa Soviet Union mu October 1991, boma linayamba kupondereza kwambiri anthu pa nkhani za ufulu wopembedza.

Chipembedzo cha Mboni za Yehova sichovomerezeka ndi malamulo m’dziko la Turkmenistan. A Mboni ena akhala akuvutika chifukwa chomenyedwa kwambiri, kuwasunga pazifukwa zosamveka, nyumba zawo kuchitidwa chipikisheni, kuwatsekera m’ndende, komanso kuwalipitsa chindapusa chifukwa chochita zimene amakhulupirira. Ena anatsekeredwapo m’ndende pamilandu yabodza yopangidwa ndi apolisi. Chifukwa choti ku Turkmenistan anthu sapatsidwa ntchito zina m’malo mwa usilikali, anyamata a Mboni amazengedwa milandu komanso kupatsidwa chilango chifukwa chokana usilikali potsatira zimene amakhulupirira. A Mboni za Yehova anakadandaula za nkhanizi ku Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu komanso ku mabungwe ena.

Mu October 2014, pulezidenti wa dziko la Turkmenistan anakhululukira a Mboni 8 omwe anawatsekera m’ndende mopanda chilungamo. A Mboni anayamikira boma la Turkmenistan chifukwa chochita zimenezi. Iwo akukhulupirira kuti boma lichitanso zinthu zina pofuna kuteteza ufulu wopembedza.