Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Akhristu a ku Kharkiv m’dziko la Ukraine, ali kumalo komwe abisala kuphulika kwa mabomba

3 MARCH, 2022
UKRAINE

Abale Akupitiriza Kusonyezana Chikondi pa Nthawi Yankhondo ku Ukraine

Abale Akupitiriza Kusonyezana Chikondi pa Nthawi Yankhondo ku Ukraine

Pa 24 February 2022, asilikali a dziko la Russia analowa m’dziko la Ukraine. Ku Ukraine kuli a Mboni za Yehova oposa 129,000 limodzi ndi ana awo. Ofesi ya nthambi inakhazikitsa Makomiti Othandiza Pangozi Zadzidzidzi okwana 27 n’cholinga choti akapereke chithandizo kwa Akhristu anzawo. Kuwonjezera pamenepa, chifukwa chokonda Akhristu anzawo, abale ndi alongo akuchita zonse zomwe angathe popereka zinthu zawo ndi kulimbikitsa abale komanso anthu ena panthawi yovutayi.

Ngakhale kuti abale ndi alongo ambiri sanatuluke m’dzikolo, ena anasankha zothawira kumayiko ena. Omwe anasankha kuthawa, anaima kwa masiku atatu kapena 4 pamizere italiitali ina yofika mpaka makilomita 30, kuti akonzetse zikalata zawo zotulukira paboda. Abale okhala m’madera akufupi, ankafufuza Akhristu anzawo omwe anali pamizereyo n’kuwapatsa chakudya, zakumwa ndi zinthu zina zofunika. Pamapeto pake abale ndi alongowa atatuluka m’dzikolo kupita kumayiko ena apafupi komwe analandiridwa ndi Amboni anzawo omwe ananyamula zikwangwani za jw.org. Abalewa anali okonzeka kupatsa Akhristu anzawo zinthu zomwe akanafunikira.

Alongo a ku Poland (kumanzere) komanso a ku Slovakia (kumanja) akudikira kuti alandire komanso kuthandiza Akhristu anzawo omwe akuthawa ku Ukraine

Mmene Zinakhudzira Abale ndi Alongo Athu

  • M’bale Petro Mozul, mtumiki wothandiza wa ku Kharkiv amene anali wosalankhula, anaphedwa pamene asilikali ankaphulitsa mabomba

    N’zomvetsa chisoni kuti pa 1 March 2022, m’bale mmodzi wosalankhula wa ku Kharkiv anaphedwa ndipo mkazi wake anavulala kwambiri chifukwa cha mabomba omwe ankaphulitsidwa

  • Alongo enanso atatu anavulala

  • Ofalitsa opitirira 5,000 anathawa m’nyumba zawo

  • Nyumba ziwiri zinawonongekeratu

  • Nyumba zitatu zinawonongeka kwambiri

  • Nyumba 35 zinawonongeka pang’ono

  • Nyumba za Ufumu ziwiri zinawonongeka

  • Ofalitsa ambiri alibe magetsi ndi madzi. Komanso matelefoni ndi zipangizo zawo zotenthetsera m’nyumba sizikugwira ntchito

Ntchito Yopereka Chithandizo

  • Kunakhazikitsidwa Makomiti Othandiza Pangozi Zadzidzidzi okwana 27

  • Ofalitsa 867 anathandizidwa ndi Makomiti Othandiza Pangozi Zadzidzidzi kuti athawire kumalo otetezeka

  • Makomiti Othandiza Pangozi Zadzidzidzi akupereka zinthu zofunika monga chakudya komanso madzi akumwa

Ziwerengerozi tinazilandira m’masiku oyambirira, nkhondoyi itayamba.

Tikupempherera abale ndi alongo athuwa kuti apitirize kuchita zinthu mwanzeru kuti akwanitse kupirira mavuto ndi zinthu zina zosayembekezereka zomwe akukumana nazo panthawi yovutayi komanso kuti apitirize kusonyezana chikondi.​—Miyambo 9:10; 1 Atesalonika 4:9.