Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Mykola Bozhedomov anaphedwa pomwe asilikali anaphulitsa siteshoni yasitima ku Kramatorsk, m’Chigawo cha Donetsk ku Ukraine

4 MAY, 2022
UKRAINE

Ankachita Zonsezi Chifukwa Cha Chikondi

“Ankafuna Kuti Umenewu Ukhale Ulendo Wake Womaliza”

Ankachita Zonsezi Chifukwa Cha Chikondi

Nkhondo itafika poipa M’chigawo cha Donetsk ku Ukraine, M’bale Mykola Bozhedomov anayenda mobwerezabwereza kupita ku Kramatorsk ndi cholinga chokathandiza anthu ambiri kuti athawire kumadera otetezeka.

Mykola ndi Nina Bozhedomov

Komabe, pa 8 April 2022, M’bale Bozhedomov yemwe anali ndi zaka 58, anaphedwa asilikali ataphulitsa siteshoni yasitima ku Kramatorsk m’Chigawo cha Donetsk.

Anthu oposa 50 anaphedwa pa chiwembuchi kuphatikizaponso mlongo mmodzi. Pa anthu oposa 100 omwe anavulala, panalinso m’bale mmodzi. Abale ndi alongo ena omwe anapulumuka pa chiwembuchi anafotokoza kuti, kunamveka chiphokoso chachikulu chifukwa cha mabomba awiri omwe anaphulika ndipo zidutswa zazitsulo zinali mbwee!

Mlongo Nina Bozhedomov wazaka 32 yemwe anali mkazi wa M’bale Bozhedomov anafotokoza kuti: “Mwamuna wanga ankaika zofuna za ena patsogolo. Iye ankafunitsitsa kuthandiza ofalitsa achikulire ndi ena omwe anali ndi mavuto a m’thupi. Ulendo uliwonse akabwerako ku Kramatorsk, ankafotokoza kuti zinthu zikuipiraipira, ndipo ankafuna kuti umenewu ukhale ulendo wake womaliza.”

M’bale ndi Mlongo Bozhedomov anabatizidwa limodzi mu 1997. M’bale Bozhedomov anatumikira mokhulupirira ngati mkulu kwa zaka zambiri. Abale ndi alongo akuyesetsa kwambiri kuthandiza ndi kulimbikitsa Mlongo Bozhedomov. Mlongoyu ananena kuti: “Mawu awo otonthoza akundilimbikitsa kwambiri pa nthawi yovutayi.”

Mlongo Nina Bozhedomov ananena kuti Malemba akumulimbikitsa kwambiri, makamaka lemba la Yesaya 40:28-31. Ananenanso kuti: “Yehova akundithandiza kuti ndipezenso mphamvu. Ndikuona kuti Yehova akundithandiza kwambiri. Poyamba ndinkangowerenga za chikondi chimenechi m’mabuku athu koma apa ndadzionera ndekha.”

Tikupempherera Mlongo Nina Bozhedomov ndi ena onse omwe aferedwa achibale ndi anzawo pa nkhondoyi. Tikudziwa kuti Yehova apitiriza kuwathandiza.—Salimo 20:2.