Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Malo a Msonkhano a ku Tiachiv, ku Ukraine, anakonzedwa kuti pazifikira anthu othawa nkhondo

8 MARCH, 2022
UKRAINE

LIPOTI #1 | Abale Akupitiriza Kusonyezana Chikondi pa Nthawi Yankhondo ku Ukraine

LIPOTI #1 | Abale Akupitiriza Kusonyezana Chikondi pa Nthawi Yankhondo ku Ukraine

Abale ndi alongo okhala m’mizinda ya Mariupol, Kharkiv, Hostomel komanso m’madera ena, akukumana ndi mavuto aakulu pomwe asilikali akupitiriza kuponya mabomba ku Ukraine. Ena atha wiki yathunthu asanatuluke m’zipinda zapansi komanso m’malo ena omwe anabisala. Pofika pano zakudya zayamba kuwathera komanso zikukhala zovuta kuti athe kulankhulana ndi anzawo chifukwa cha vuto la kuthima kwa magetsi komanso chifukwa choti netiweki sikugwira.

N’zomvetsa chisoni kuti M’bale Dmytro Rozdorskyi, mkulu wazaka 28 yemwe ankakhala ku Myrnohrad, anafa ataponda bomba. Tikupempherera onse omwe aferedwa achibale ndi anzawo. Tikupemphereranso abale ndi alongo athu omwe ali m’madera omwe kukuphulitsidwa mabomba.​—2 Atesalonika 3:1.

Nyumba ya Ufumu ya m’tawuni ya Ovruch, ku Ukraine, inawonongeka kwambiri ndi mabomba

Pofika pa 7 March 2022, tinalandira lipoti lotsatirali kuchokera ku Ukraine:

Mmene Zinakhudzira Abale ndi Alongo Athu

  • Ofalitsa awiri anafa

  • Ofalitsa 8 anavulala

  • Ofalitsa 20,617 anathawa m’nyumba zawo n’kupita kumadera ena m’dziko lomwelo

  • Nyumba 25 zinawonongekeratu

  • Nyumba 29 zinawonongeka kwambiri

  • Nyumba 173 zinawonongeka pang’ono

  • Nyumba za Ufumu 5 zinawonongeka

Ntchito Yopereka Chithandizo

  • Kunakhazikitsidwa Makomiti Othandiza pa Ngozi Zadzidzidzi okwana 27

  • Ofalitsa 6,548 anathandizidwa ndi makomitiwa kuti athawire kumalo otetezeka

  • Ofalitsa 7,008 anathawira kumayiko ena ndipo akuthandizidwa ndi Akhristu anzawo

  • Malo a Msonkhano amodzi komanso Nyumba za Ufumu 30 za m’chigawo chakumadzulo kwa Ukraine monga ku Chernevtsi, Ivano-Frankivsk, Lviv ndi ku m’madera a ku Transcarpathian, zinakonzedwa kuti kuzifikira anthu othawa nkhondo