Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Mlongo Olena ali kutsogolo kwa nyumba yake yomwe inawonongeka ndi bomba. Nthawi yomweyo abale anafika kuti adzamuthandize

4 JULY, 2022
UKRAINE

LIPOTI #10 | Abale Akupitiriza Kusonyezana Chikondi pa Nthawi Yankhondo ku Ukraine

Zitsanzo za Anthu “Olimba Mtima, Odera Nkhawa Ena Komanso Odalirika”

LIPOTI #10 | Abale Akupitiriza Kusonyezana Chikondi pa Nthawi Yankhondo ku Ukraine

Abale ndi alongo athu a ku Ukraine sanasiye kuthandiza Akhristu anzawo. Akupitirizabe kusonyezana chikondi mmalo mongoganizira zofuna zawo zokha.

Mlongo Olena ali ndi zaka 81. Pa 6 June, bomba linaphulika pafupi kwambiri ndi nyumba yake. Bombalo linawonongeratu nyumba ya neba wake ndipo pamalopo panakumbika chidzenje chachikulu chokwana mamita 7. Linali bomba lamphamvu kwambiri moti nyumba ya Mlongo Olena inawonongeka kwambiri.

Mlongoyu ananena kuti: “Panthawiyo ndinali ndikugona ndipo khoma linagwera pafupi ndi kumutu kwanga. Kunali fumbi lokhalokha. Magalasi ndi miyala zinali mbwee paliponse. Ndinathokoza Yehova kuti ndinapulumuka.” Patangotha maminitsi ochepa, abale ndi alongo anabwera kudzaona Mlongo Olena. Pagululo panali m’bale wina amenenso nyumba yake inawonongeka kwambiri. Mlongo Olena anapitiriza kunena kuti: Abale ndi alongo atafika, anangoti kukamwa yasa kusowa chonena. Ndinalimbikitsidwa kwambiri ndi kubwera kwawo. Zinali zosangalatsa kwambiri kuti anali nane pafupi pa nthawi yovutayi.

M’bale Serhii ndi mkulu ndipo amakonda kuyendera Mlongo Olena ali limodzi ndi achinyamata ena a mumpingo wawo. Iye ananena kuti: “Nditangomva kuti kwaphulika bomba pafupi ndi nyumba ya Mlongo Olena, ndinachita mantha komanso ndinali ndi nkhawa. Mtima unakhalako m’malo nditaona kuti anangosupukasupuka koma sanavulale modetsa nkhawa. Chodabwitsa n’chakuti chinthu choyambirira chomwe Mlongo Olena anafuna nyumba yake itawonongeka, chinali buku lofotokoza nkhani za m’Baibulo lomwe anali atangolandira masiku kumene.”

Zinali zosangalatsa kuti achibale ake anamupezeranso nyumba ina. Abale ndi alongo akupitiriza kuthandiza mlongoyu ndipo akulu amayesetsa kulankhula naye tsiku lililonse. Abale ndi alongo anamupezera zipangizo zothandizira kumva kuti azipindula akakhala pamisonkhano. Mlongoyu anafotokoza kuti: “Nthawi zina ndimakhala wofooka, koma misonkhano imandipatsa mphamvu. Akhristu anzanga amandiimbira foni pafupipafupi ndipo ndimathokoza kwambiri chifukwa cha zimenezi.”

Banja lina linafotokoza mmene zinthu zinalili pomwe anabisala m’chipinda chapansi panthaka mu Nyumba ya Ufumu limodzi ndi ofalitsa ena okwana 200. Mlongo wa m’banjali anati: “Ndinachita chidwi kwambiri ndi mmene akulu achikondi ankatisamalirira. Zomwe ankachita zinandikumbutsa nkhani ya Davide yemwe anaika moyo wake pa ngozi pomenyana ndi mkango komanso chimbalangondo ndi cholinga chofuna kupulumutsa nkhosa. Akulu omwe tinkakhala nawo m’chipinda chapansi panthaka ankaika moyo wawo pa ngozi kuti akapeze chakudya ndi madzi komanso petulo wolizira jenereta kuti tikhale ndi magetsi. Chifukwa cha zimenezi tinkakwanitsa kuchita misonkhano yampingo komanso yokonzekera utumiki. Ngakhale pomwe asilikali akuponya mabomba, nthawi zonse akuluwa ankayenderabe abale ndi alongo omwe anali m’nyumba zawo, kukawapatsa chakudya ndi madzi komanso kukawalimbikitsa. Akuluwa ndimawapatsa ulemu waukulu. Nkhondoyi isanafike, ndinkangowadziwa monga aphunzitsi komanso ogwira ntchito yolalikira. Koma panopo ndimawaona kuti ndi abusa odalirika. Ndimayamikira kuti akuluwa ndi zitsanzo za anthu “olimba mtima, odera nkhawa ena komanso odalirika.”

Ofalitsa a mpingo wina ku Ukraine analembera kalata ofesi ya nthambi pofuna kuwafotokozera ntchito yomwe akulu akugwira pa nkhani yopereka chithandizo. Iwo ananena kuti; “Ndife oyamikira kwambiri. Tikugoma ndi mmene Yehova akutisamalirira pogwiritsa ntchito Akhristu anzathu. Tikutsimikizira mawu omwe Yesu ananena akuti: ‘Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.’—Yohane 13:35.”

Pofika pa 21 June 2022, tinalandira malipoti otsatirawa kuchokera ku Ukraine. Ziwerengerozi zinatsimikiziridwa ndi abale a m’dzikolo. Komabe n’kutheka kuti ziwerengerozi ndi zokwera kwambiri kuposa pamenepa chifukwa sitikutha kulankhulana ndi abale a m’zigawo zonse za dzikolo.

Mmene Zakhudzira Abale ndi Alongo Athu

  • Ofalitsa 42 anafa

  • Ofalitsa 83 anavulala

  • Ofalitsa 31,185 anathawa m’nyumba zawo n’kupita kumadera otetezeka

  • Nyumba 495 zinawonongekeratu

  • Nyumba 557 zinawonongeka kwambiri

  • Nyumba 1,429 zinawonongeka pang’ono

  • Nyumba za Ufumu 5 zinawonongeka kwambiri

  • Nyumba za Ufumu 8 zinawonongeka kwambiri

  • Nyumba za Ufumu 34 zinawonongeka pang’ono

Ntchito Yopereka Chithandizo

  • Pali Makomiti Othandiza pa Ngozi Zadzidzidzi okwana 27 omwe akugwira ntchito ku Ukraine

  • Anthu 52,348 anathandizidwa ndi makomitiwa kuti athawire kumalo otetezeka

  • Ofalitsa 23,433 anathawira kumayiko ena komwe akuthandizidwa ndi Akhristu anzawo