Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Ofalitsa awiri akulalikira m’malo opezeka anthu ambiri ku Ukraine

18 JULY, 2022
UKRAINE

LIPOTI #11 | Abale Akupitiriza Kusonyezana Chikondi pa Nthawi Yankhondo ku Ukraine

“Kuchita Zabwino” M’dziko la Nkhondo

LIPOTI #11 | Abale Akupitiriza Kusonyezana Chikondi pa Nthawi Yankhondo ku Ukraine

Abale ndi alongo onse ku Ukraine asangalala kuti ayambiranso kulalikira m’malo opezeka anthu ambiri ndipo ntchitoyi yakhala ndi zotsatirapo zabwino kwambiri. Oyang’anira madera ndi akulu a m’mipingo afotokoza kuti anthu ambiri asangalala kuona timashelefu tathu titabwereranso m’misewu. Moti ena ananena kuti anawasowa kwambiri a Mboni za Yehova.

Tatiana wochokera mu Mpingo wa Serhiivka m’chigawo cha Odesa, anakayendera anthu omwe anakumanapo nawo m’mbuyomo mliri usanayambe. Iye anafotokoza kuti, “Titangoyambiranso kulalikira, ndinaona kuti Yehova akudalitsa kwambiri ntchitoyi.” Tsiku lina Tatiana, anapita kunyumba kwa mayi wina amene nthawi ina mliri usanayambe, anakana kuti aziphunzira Baibulo. Koma pa ulendowu mayiyo anavomera kuti azikambirana naye nkhani zauzimu komanso mwamsanga anavomera kuti aziphunzira naye Baibulo. Tatiana anamaliza ndi kunena kuti, “Panopo ndikufuna kuyendera anthu onse omwe ndinkawalalikira kuti ndikawapemphe ngati ndingayambe kuphunzira nawo Baibulo.”

Yevheniy ndi Lilia kwawo kwenikweni ndi ku Mariupol. Ofalitsawa anathawa kwawo ndipo pano akukhala m’dera lina lotetezeka ku Ukraine komweko. Iwo amakonda kulalikira nthawi zambiri. Iwo anafotokoza kuti kulowa muutumiki kwawathandiza kuti asamangokhalira kuganizira mavuto omwe akukumana nawo. Iwo anati: “Tinkadziwa kuti moyo sudzakhala chimodzimodzi. Ndi zovuta kwambiri kuzolowera moyo watsopanowu komabe timakumbukira kuti Yehova sangatisiye. Iye amatithandiza ndi mzimu wake komanso tili ndi Akhristu anzathu omwe ndi okonzeka kutithandiza kuti tizolowere moyo watsopano kudera lachilendo.”

M’madera enanso a ku Ukraine, abale athu akuchitira umboni pochita ntchito zabwino. Mwachitsanzo, gulu lina la abale mumzinda wa Mykolaiv linathandiza bungwe lina lopereka chithandizo kwa anthu ovutika powakonzera nyumba yomwe ankasungiramo katundu. Abalewa anakonza mapaipi a madzi, mashelefu komanso kusanja katundu yemwe analipo wambiri. Woyang’anira ntchito za bungwelo atabwera, anasangalala kwambiri ndi mmene abalewa anagwirira ntchitoyo mpaka anagwetsa misozi. Iye ananena kuti: “Sindinayembekezere kuti mungagwire ntchito yabwino chonchi.”

Ngakhale kuti abale athu a ku Ukraine akukumana ndi mavuto ambiri, akukhalabe osangalala chifukwa chochitabe khama pa ntchito yolalikira komanso chifukwa ‘chochita zabwino.’—Agalatiya 6:9.

Pofika pa 13 July 2022, tinalandira malipoti otsatirawa kuchokera ku Ukraine. Ziwerengerozi zinatsimikiziridwa ndi abale a m’dzikolo. Komabe n’kutheka kuti ziwerengerozi ndi zokwera kwambiri kuposa pamenepa chifukwa sitikutha kulankhulana ndi abale a m’zigawo zonse za dzikolo.

Mmene Zakhudzira Abale ndi Alongo Athu

  • Ofalitsa 42 anafa

  • Ofalitsa 97 anavulala

  • Ofalitsa 28,683 anathawa m’nyumba zawo n’kupita kumadera otetezeka

  • Nyumba 524 zinawonongekeratu

  • Nyumba 588 zinawonongeka kwambiri

  • Nyumba 1,554 zinawonongeka pang’ono

  • Nyumba za Ufumu 5 zinawonongekeratu

  • Nyumba za Ufumu 10 zinawonongeka kwambiri

  • Nyumba za Ufumu 36 zinawonongeka pang’ono

Ntchito Yopereka Chithandizo

  • Pali Makomiti Othandiza pa Ngozi Zadzidzidzi okwana 27 omwe akugwira ntchito ku Ukraine

  • Anthu 52,947 anathandizidwa ndi makomitiwa kuti athawire kumalo otetezeka

  • Ofalitsa 23,863 anathawira kumayiko ena komwe akuthandizidwa ndi Akhristu anzawo