Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Maubatizo awiri omwe anachitika ku Ukraine pa 23 July, 2022

12 AUGUST, 2022
UKRAINE

LIPOTI #12 | Abale Akupitiriza Kusonyezana Chikondi pa Nthawi Yankhondo ku Ukraine

“Ngakhale Nkhondo Siingaimitse Ntchito Yophunzitsa Anthu Kuti Akhale Otsatira a Yesu”

LIPOTI #12 | Abale Akupitiriza Kusonyezana Chikondi pa Nthawi Yankhondo ku Ukraine

Kuyambira pa 23 mpaka pa 31 July, ofalitsa a ku Ukraine komanso m’mayiko omwe anathawira anabatizidwa pa Msonkhano wa 2022 wakuti “Yesetsani Kukhala Mwamtendere.” Pofika pa 2 August, anthu okwana 1,113 a ku Ukraine anabatizidwa. M’bale wina ku Ukraine ananena kuti: “Ngakhale nkhondo siingaimitse ntchito yophunzitsa anthu kuti akhale otsatira a Yesu mogwirizana ndi zomwe mwini wake analonjeza kuti: ‘Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse.’—Mateyu 28:20.

Ndife osangalala kukudziwitsani zinthu zotsatirazi zomwe zachitika.

Natalia wa ku Kreminna m’Chigawo cha Luhansk, ali ndi zaka 63. Iye ndi ana ake aakazi awiri anayamba kuphunzira ndi Mboni za Yehova m’zaka za m’ma 1990. Ana ake okha ndi amene anapita patsogolo mwauzimu n’kubatizidwa. Nkhondo itangoyamba, banja lina la Mboni za Yehova linatenga Natalia pomwe linkathawa nkhondo. Natalia anayamba kukhala nawo m’Nyumba ya Ufumu ina ku Ivano-Frankivsk.

Natalia anafotokoza kuti: “Chifukwa cha mabomba oopsa omwe anaphulitsidwa m’dera lathu, sindinkakhalanso wosangalala. Abale ndi alongo anandisonyeza chikondi chenicheni. Sindinayembekezere kuti angandichitire zimenezi. Pa nthawiyi ndinayambiranso kukonda Yehova. Ndinkawerenga Baibulo kwambiri ndipo mlongo wina anayamba kuphunzira nane Baibulo pogwiritsa ntchito buku lakuti, Mungakhale ndi Moyo Mpaka Kalekale. Osanama, mlongoyu anali mphatso yochokera kwa Yehova.” Natalia anapitiriza kufotokoza kuti: “Panopo ndine wosangalala kwambiri kuti ndabatizidwa kukhala wa Mboni za Yehova. Ndikufunitsitsa kutsatira lamulo lofunika kwambiri kuti ndizikonda Yehova Mulungu wanga ndi ‘mtima wanga wonse, moyo wanga wonse, ndi maganizo anga onse.’”—Mateyu 22:37.

Ku Poland, Olia wanyamula pepala lokhala ndi mutu wa msonkhano wakuti: “Yesetsani Kukhala Mwamtendere”

Olia wa ku Cherkasy, anali wofalitsa wosabatizidwa pomwe nkhondo inkayamba. Pa 6 March, iye anathawira m’dziko la Poland ndi mwana wake wamkazi komanso mdzukulu wake. Iye anafotokoza kuti: “Tinafika ku Poland chimanjamanja tili ndi kachikwama kapangozi basi. Koma abale ndi alongo anatisamalira kwambiri. Zimenezi zinanditsimikizira kuti gulu la Yehova ndi logwirizana komanso kuti likutsogoleredwadi ndi mzimu wake. Chifukwa choganizira mmene abale ndi alongo ankatisamalirira, ndinatsimikiza mtima kuti ndidzipereke kwa Yehova. Iye anandithandiza pa nthawi yovuta kwambiri ndipo inenso ndikufuna kuyamba kumutumikira monga njira yosonyezera kumuyamikira pa zomwe anandichitira.”

Yulia amene ndi wochokera m’Chigawo cha Donetsk, ali ndi zaka 18. Iye analeredwa m’banja la Mboni koma sanapite patsogolo kuti abatizidwe. Yulia akufotokoza zimene zinamuchitikira nkhondo itangotsala pang’ono kuyamba. Iye anafotokoza kuti: “M’dera lomwe banja lathu tinkakhala, paliponse panawonongedwa ndi mabomba, koma mwamwayi tinapulumuka. Nditaganizira zomwe zinachitikazi, kupemphera komanso kuganizira mozama za makhalidwe a Yehova, ubwenzi wanga ndi iye unalimba kwambiri ndipo ndinasiya kukayikira zoti ndidzipereke kwa Yehova. Atayankha mapemphero anga, ndinatsimikiza kuti Yehova anali nane pafupi. Poyamba ndinkangodziwa zokhudza Yehova koma panopo ndimakukonda kwambiri.” Yulia anabatizidwa pa 23 July.

David wazaka 11, atangotsala pang’ono kubatizidwa ku Germany

Nkhondo itangoyamba, David wazaka 11 anathawira ku Germany limodzi ndi banja lawo. Iye anakhala wofalitsa wosabatizidwa atangokwanitsa zaka 9. Tsopano ndi wofunitsitsa kuti akwaniritse zolinga zake zauzimu. Iye anafotokoza kuti: “Ndinaganiza zoti ndibatizidwe chifukwa ndimakonda Yehova ndipo ndimafuna kuti ndikhale mnzake. Pomwe ndinkabatizidwa ndinalira chifukwa chosangalala nditadziwa kuti tsopano ndili m’banja la Yehova. Ndimakonda kuuza anthu ena zokhudza Yehova koma za cholinga chake chokhudza anthufe. Choncho cholinga changa china chomwe ndikufuna kuchikwaniritsa tsopano, ndikuchita upainiya. Ndikufunanso kuti ndizitumikira abale ndi alongo mumpingo wathu ndipo ndikukhulupirira kuti nthawi ina ndidzakhala mtumiki wothandiza. Cholinga changa chachikulu ndi chofuna kudzatumikira pabeteli. Ndinayamba kuganizira zotumikira pabeteli kungoyambira pomwe tinakayendera ofesi ya nthambi ku Lviv mu 2018.”

Olena wa ku Kyiv anakhala wofalitsa wosabatizidwa mu 2011. Koma anasiya kuchita zinthu zauzimu kwa zaka 10. Mu 2020 akulu anamupeza n’kumupatsa kabuku kakuti, Bwererani kwa Yehova. Iye anafotokoza kuti: “Ndinayambiranso kuphunzira Baibulo komanso kupezeka pamisonkhano. Komabe patapita nthawi ndinasiyanso. Pa nthawi yankhondo, Yehova anayankha mapemphero anga ndipo ndinaona kuti Yehova ananditeteza, anandisonyeza chikondi komanso anandipatsa mtendere wamumtima. Ndinathawira ku Romania ndipo ndinakakumana ndi abale. Abale anandisamalira mwachikondi ndipo zinali ngati kuti Yehova wandifunditsa bulangete lotenthera bwino.” Olena anabatizidwa pa 23 July. Iye anamaliza ndi kunena kuti: “Ndimathokoza Yehova chifukwa choleza nane mtima. Tsopano ndimaona kuti ‘ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.’”—Afilipi 4:13.

Pofika pa 2 August 2022, tinalandira malipoti otsatirawa kuchokera ku Ukraine. Ziwerengerozi zinatsimikiziridwa ndi abale a m’dzikolo. Komabe n’kutheka kuti ziwerengerozi ndi zokwera kwambiri kuposa pamenepa chifukwa sitikutha kulankhulana ndi abale a m’zigawo zonse za dzikolo.

Mmene Zakhudzira Abale ndi Alongo Athu

  • Ofalitsa 43 anafa

  • Ofalitsa 97 anavulala

  • Ofalitsa 22,568 anathawa m’nyumba zawo n’kupita kumadera otetezeka

  • Nyumba 586 zinawonongekeratu

  • Nyumba 613 zinawonongeka kwambiri

  • Nyumba 1,632 zinawonongeka pang’ono

  • Nyumba za Ufumu 5 zinawonongekeratu

  • Nyumba za Ufumu 10 zinawonongeka kwambiri

  • Nyumba za Ufumu 37 zinawonongeka pang’ono

Ntchito Yopereka Chithandizo

  • Pali Makomiti Othandiza pa Ngozi Zadzidzidzi okwana 27 omwe akugwira ntchito ku Ukraine

  • Anthu 53,836 anathandizidwa ndi makomitiwa kuti athawire kumalo otetezeka

  • Ofalitsa 24,867 anathawira kumayiko ena komwe akuthandizidwa ndi Akhristu anzawo