Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

16 NOVEMBER, 2022
UKRAINE

LIPOTI #13 | Abale Akupitiriza Kukondana pa Nthawi Yankhondo ku Ukraine

Kuyambiranso Kulalikira Pamasom’pamaso

LIPOTI #13 | Abale Akupitiriza Kukondana pa Nthawi Yankhondo ku Ukraine

Mu August 2022, panaperekedwa chilengezo chakuti abale akhoza kuyambiranso kulalikira kunyumba ndi nyumba kumadera a ku Ukraine omwe kuli chitetezo. Abale ndi alongo athu anagwira nawo ntchitoyi mofunitsitsa. Ndipo anaona kuti anthu ambiri anali ndi chidwi kuti amvetsere uthenga wa m’Baibulo. Mmodzi mwa anthu amene anavomera kuphunzira Baibulo ananena kuti: “Pambuyo poona zinthu zoopsa komanso kuvutika pa nthawi ya nkhondoyi, zaonetseratu kuti ndi Mulungu yekha yemwe angathetse mavuto a anthu.” Zotsatirazi ndi zimene abale ndi alongo ena anakumana nazo muutumiki.

A Ruslan a mumpingo wa Lanivtsi, ankachita mantha kuti ayambirenso kulalikira kunyumba ndi nyumba. Iwo limodzi ndi mkazi wawo, anapemphera kwa Yehova kuti awathandize kukhala olimba komanso awatsogolere kwa anthu amene ali ndi chidwi chokhala ndi chiyembekezo cha tsogolo labwino. Iwo anadabwa kuona kuti kwa maola awiri oyambirira omwe analalikira, analankhulana ndi athu 8 ndipo onse anavomera kuphunzira Baibulo.

Mlongo Olha wa mumpingo wa Kremenets ali mu utumiki ndi nzake, bambo wina anawathamangira ndi kuwafunsa ngati akuuza anthu za uthenga wa Mulungu. Bamboyo ananena kuti: “Ndimasuta fodya komanso ndimavutika chifukwa cha mowa. Ndikudziwa kuti posachedwa Mulungu adzandiweruza. Ndipo sindikufuna kuti pa nthawiyo ndidzakhale mmene ndilili panopa.” Ndipo panakonzedwa zoti abale a m’dera lomwe bamboyo amakhala azipita kukaphunzira naye Baibulo.

Panthawi imene ankalalikira limodzi ndi kagulu kake ka utumiki, M’bale Vasyl wa mumpingo wa Lviv-Riasne-Skhidnyi anakumbukira za nyumba ya mzimayi wina yemwe anamulalikira zaka zingapo zapitazo. Iye anakumbukira kuti mzimayiyo, mokwiya anakanitsitsa kulankhula ndi a Mboni za Yehova. Iye anasankha kugogoda pakhomopo ndi cholinga chopempha mwini nyumbayo kuti aziphunzira naye Baibulo. M’bale Vasyl anadabwa kuona kuti mzimayi yemwe uja watuluka pakhomopo ndipo ananena kuti akufuna kumvetsa Malemba Opatulika. Mzimayiyo anavomera kuphunzira Baibulo ndipo abale anakonza zoti munthu wina azikaphunzira naye.

M’bale Serhii wa mumpingo wa Illintsi yemwe anabatizidwa mu 2021, anali asanagwirepo ntchito yolalikira kunyumba ndi nyumba. Iye ankachita mantha kwambiri, choncho anapeza nthawi yokonzekera. Iye ananena kuti: “Ndinaonera mavidiyo a zitsanzo za ulaliki ma ulendo angapo. Pambuyo pake chomwe ndinkafunikira ndi kulimbikitsidwa basi.” Mosangalala M’bale Serhii ananena kuti nkhawa yake inasanduka chisangalalo chifukwa cha mwayi womwe anali nawo wouza ena uthenga wabwino.

Nayenso Nikol wa mumpingo wa Rozdil yemwe anakhala wofalitsa wosabatizidwa mu August 2022, ananena kuti: “Ndinkachita mantha kwambiri komanso ndinali ndi nkhawa ndikaganizira zolalikira pamasom’pamaso. Komabe nditangoyamba kulalikira, ndinaona mmene zimasangalatsira kuuza ena zokhudza Yehova pamasom’pamaso.”

Alongo awiri akulalikira kunyumba ndi nyumba

Pofika pa 11 November 2022, tinalandira malipoti otsatirawa kuchokera ku Ukraine. Ziwerengerozi zinatsimikiziridwa ndi abale a m’dzikolo. Komabe n’kutheka kuti ziwerengerozi ndi zokwera kwambiri kuposa pamenepa chifukwa sitikutha kulankhulana ndi abale a m’zigawo zonse za dzikolo.

Mmene Zakhudzira Abale ndi Alongo Athu

  • Ofalitsa 46 anafa

  • Ofalitsa 97 anavulala

  • Ofalitsa 12,569 anathawa m’nyumba zawo

  • Nyumba 590 zinawonongekeratu

  • Nyumba 645 zinawonongeka kwambiri

  • Nyumba 1,722 zinawonongeka pang’ono

  • Nyumba za Ufumu 6 zinawonongekeratu

  • Nyumba za Ufumu 19 zinawonongeka kwambiri

  • Nyumba za Ufumu 63 zinawonongeka pang’ono

Ntchito Yopereka Chithandizo

  • Pali Makomiti Othandiza pa Ngozi za Mwadzidzidzi okwana 27 omwe akugwira ntchito ku Ukraine

  • Anthu 53,948 anathandizidwa ndi makomitiwa kuti athawire kumalo otetezeka

  • Ofalitsa 25,983 anathawira kumayiko ena komwe akuthandizidwa ndi Akhristu anzawo