20 DECEMBER 2022
UKRAINE
LIPOTI #14 | Abale Akupitiriza Kukondana pa Nthawi Yankhondo ku Ukraine
Zinthu zambiri za ku Ukraine monga misewu, mabiliji komanso malo opanga magetsi zaonongeka kapena kuonongekeratu chifukwa cha mabomba amene akuphulika kawirikawiri. Ngakhale zili choncho, abale athu sanasiyebe kupezeka pamisonkhano komanso kugwira nawo ntchito za Ufumu ngakhale kuti nthawi zambiri kukumakhala kopanda magetsi.
Anastasia ndi Debora omwe amachita upainiya ku Kyiv, ananena kuti amakhala tsiku lonse lathunthu opanda magetsi. Amatchaja zipangizo zawo zamakono pa nthawi yomwe angakwanitse komanso kugwiritsa ntchito mayunitsi amufoni yawo kuti azipezeka pamisonkhano. Nthawi zambiri Intaneti imavuta kwambiri misonkhano ikatha.
Vuto linanso lomwe amakumana nalo chifukwa cha kuzima kwa magetsi ndi kuvutika kugwiritsira ntchito zipangizo zotenthetsera mpweya. Kuti akhale ndi magetsi komanso kugwiritsira ntchito zipangizo zotenthetsera mpweya, ena mwa abale akumagwiritsa ntchito majenereta. Ndipo abale ena akukhala ndi achibale awo omwe ali ndi zotenthetsera mpweya m’nyumba zawo pomwe ena amapirira kuzizirako. Koma chosangalatsa n’chakuti m’nyumba zambiri za abale muli zipangizo zotenthetsera mpweya zomwe amagwiritsa ntchito gasi, choncho sizidalira magetsi.
Iryna yemwe ndi mpainiya ku Ivano-Frankivsk, amayesetsa kuona zinthu moyenerera. Iye ananena kuti, “Ndinaganiza zoti ndisamaganizire kwambiri za zinthu zimene sindingathe kuzisintha. Ndiye ndimangochita zomwe ndingathe paola limenelo basi. Ndimaganizira zomwe ndingachite pa nthawi yomwe magetsi azima ndipo ndimaonetsetsa kuti ndapangiratu dawunilodi mabuku ndi zinthu zina zofunikira pasadakhale.”
Ngakhale kuti abale ndi alongo athu akukumana ndi mavuto ambiri ku Ukraine, iwo akuyesetsabe kuchita zambiri potumikira Yehova. Ndife otsimikiza kuti Iye apitiriza kudalitsa khama lawo pomwe ‘akuchita zabwino.’—Agalatiya 6:9.
Pofika pa 6 December 2022, tinalandira malipoti otsatirawa kuchokera ku Ukraine. Ziwerengerozi zinatsimikiziridwa ndi abale am’dzikolo. Komabe n’kutheka kuti ziwerengerozi ndi zokwera kwambiri kuposa pamenepa chifukwa sitikutha kulankhulana ndi abale am’zigawo zonse za dzikolo.
Mmene Zakhudzira Abale ndi Alongo Athu
Ofalitsa 47 anafa
Ofalitsa 97 anavulala
Ofalitsa 11,537 anathawa m’nyumba zawo
Nyumba 590 zinawonongekeratu
Nyumba 645 zinawonongeka kwambiri
Nyumba 1,722 zinawonongeka pang’ono
Nyumba za Ufumu 7 zinawonongekeratu
Nyumba za Ufumu 19 zinawonongeka kwambiri
Nyumba za Ufumu 68 zinaonongeka pang’ono
Ntchito Yopereka Chithandizo
Pali Makomiti Othandiza pa Ngozi za Mwadzidzidzi okwana 27 omwe akugwira ntchito ku Ukraine
Anthu 54,212 anathandizidwa ndi makomitiwa kuti athawire kumalo otetezeka
Ofalitsa 26,811 anathawira kumayiko ena komwe akuthandizidwa ndi Akhristu anzawo