Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Abale ongodzipereka ogwira ntchito zomangamanga akukonza nyumba kumadera omwe ali otetezeka

29 DECEMBER 2022
UKRAINE

LIPOTI #15 | Abale Akupitiriza Kukondana pa Nthawi Yankhondo ku Ukraine

LIPOTI #15 | Abale Akupitiriza Kukondana pa Nthawi Yankhondo ku Ukraine

Kungoyambira mu February 2022 pomwe nkhondo inayamba ku Ukraine, nyumba za a Mboni za Yehova zokwana 3,000 zinawonongeka kapena kuwonongekeratu. Moyang’aniridwa ndi Dipatimenti Yothandiza Pakachitika Ngozi Zadzidzidzi komanso Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga, abale ku Ukraine anayamba kukonza nyumba kumadera omwe kuli chitetezo. Ntchitoyi ikuphatikizapo kukonza denga lowonongeka komanso mawindo ndi zinthu zina. Nthawi zina nyumba ikawonongekeratu, malo oimikapo magalimoto amakonzedwa kuti akhale nyumba yaing’ono. Pofika panopa, amaliza mapulojekiti okwana 37 ndipo enanso 48 ali mkati.

Ndi zovuta kwambiri kukonzanso nyumbazi pa nthawi ya ziwawa ngati zimenezi. Komabe, abale sanasiye kugwira nawo ntchito yopereka chithandizo. Mlongo Svitlana wazaka 70, yemwe amachokera ku Velyka Dymerka, m’chigawo cha Kyiv, ananena kuti: “Ndinalibe ndalama zokwanira kuti ndikonze denga la nyumba komanso kutsogolo kwa nyumba yanga. Koma Yehova anandichitira zinthu zodabwitsa. Abale anabwera ndi kumalizitsa ntchito yonse kwa masiku atatu okha.”

Mlongo Nadiia wa ku Horenka, m’chigawo cha Kyiv, ananena kuti ntchito yopereka chithandizo inathandiza kwambiri mu utumiki. Iye anati: “Ntchito yokonzanso nyumba za abale yachitira umboni kwa wina aliyense. Ngakhale anthu omwe sindimawadziwa akulankhula za chikondi chenicheni chomwe a Mboni za Yehova amasonyezana pakati pawo. Iwo samayembekezera kuti abale angabwere kudzandithandiza.”

Ngakhale abale omwe nyumba zawo zinawonongeka akuthandiza ena, ngati mmene zilili ndi a Yevhen ndi a Tetiana. Nyumba ya banjali inawonongekeratu bomba litaphulika. M’malo momangoganizira zinthu zawo zomwe zawonongeka, iwo akugwira ntchito mwakhama kuthandiza abale ndi alongo. A Yevhen ananena kuti: “Nthawi zonse cholinga chathu chimakhala kuthandiza ena. Kuthandiza ena kumatithandizanso kuti tizipirira mavuto athu.”

Nyumba yomwe inawonongeka komanso itakonzedwa ku Velyka Dymerka, m’chigawo cha Kyiv

Mofanana ndi zimenezi, abale atakonza nyumba ya Mlongo Lidiia ku Hostomel, m’chigawo cha Kyiv, nayenso analimbikitsidwa kuti akathandize nawo pa ntchito yopereka chithandizo. Iye ananena kuti: “Kwa mawiki awiri, abale ndi alongo 16 anagwira ntchito yokonza nyumba yanga. Ndinamva ngati ndalowa kale m’dziko latsopano. Ndipo panopa ndikufuna kuthandizanso ena.”

Posachedwapa m’bale wa m’Komiti ya Nthambi ku Ukraine anakafika kumadera omwe kukugwiridwa ntchito yopereka chithandizo n’cholinga chokalimbikitsa abale ndi alongo omwe nyumba zawo zinawonongeka. Iye ananena kuti: “Nthawi zonse abale a ku Ukraine akhala akusonyeza chitsanzo chabwino pa nkhani yosonyezana chikondi. Komabe, nkhondoyi yapangitsa kuti tikhale ogwirizana kwambiri. Ndi zolimbikitsa kuona kuti thandizo limene abale akhala akulandira lawathandiza kuti azichita zambiri mu utumiki komanso lawathandiza kuti ‘azipereka mapemphero ochuluka oyamika Mulungu’ ngati mmene lemba la 2 Akorinto 9:12 limanenera.”

Pofika pa 20 December 2022, tinalandira malipoti otsatirawa kuchokera ku Ukraine. Ziwerengerozi zinatsimikiziridwa ndi abale am’dzikolo. Komabe n’kutheka kuti ziwerengerozi ndi zokwera kwambiri kuposa pamenepa chifukwa sitikutha kulankhulana ndi abale am’zigawo zonse za dzikolo.

Mmene Zakhudzira Abale ndi Alongo Athu

  • Ofalitsa 47 anafa

  • Ofalitsa 97 anavulala

  • Ofalitsa 11,477 anathawa m’nyumba zawo

  • Nyumba 590 zinawonongekeratu

  • Nyumba 645 zinawonongeka kwambiri

  • Nyumba 1,722 zinawonongeka pang’ono

  • Nyumba za Ufumu 7 zinawonongekeratu

  • Nyumba za Ufumu 19 zinawonongeka kwambiri

  • Nyumba za Ufumu 68 zinawonongeka pang’ono

Ntchito Yopereka Chithandizo

  • Pali Makomiti Othandiza pa Ngozi za Mwadzidzidzi okwana 26 omwe akugwira ntchito ku Ukraine

  • Anthu 54,212 anathandizidwa ndi makomitiwa kuti athawire kumalo otetezeka

  • Ofalitsa 26,892 anathawira kumayiko ena komwe akuthandizidwa ndi Akhristu anzawo