1 FEBRUARY 2023
UKRAINE
LIPOTI #16 | Abale Akupitiriza Kukondana pa Nthawi Yankhondo ku Ukraine
Kuyambiranso Kuchita Sukulu ya Utumiki Waupainiya
Kungoyambira pa 26 December 2022, apainiya apadera ndi okhazikika anayamba kuchita Sukulu ya Utumiki Waupainiya m’madera omwe anali otetezeka kuchita zimenezi. Potengera dera lomwe akukhala, apainiyawa ankachita sukuluyi pamasom’pamaso kapena kudzera pa Zoom. Ngakhale kuti abale ndi alongo athu ankakumana ndi mavuto monga phokoso la masayilini ochenjeza anthu, kuzima kwa magetsi, kusowa kwa ndalama komanso mavuto a Intaneti, iwo ankaona kuti ndi zofunika kwambiri kulandira maphunziro apaderawa. Kuchita zimenezi kwawathandiza kuti apitirize kukonda kwambiri Yehova komanso chikhulupiriro chawo chalimba kwambiri.
Natalia yemwe amakhala ku Kryvyi Rih, ananena kuti: “Kwa ine sukuluyi inali ngati chinthu chopangitsa munthu kuti asamire ndi madzi. Yandithandiza kuti ndisamire ndi nkhawa komanso mantha.” Nayenso Anastasia wa ku Chernivtsi, ananena kuti: “Sukuluyi yandithandiza kutsimikizira kuti Yehova amandikonda kwambiri. Chaka chapitachi, panachitika zinthu zambiri zoopsa, koma sukuluyi inali ya pa nthawi yake. Ndiyesetsa kuchita zonse zomwe ndingathe kuti Yehova apitirize kundidalitsa.”
Mlongo Svitlana, yemwe ndi mpainiya ku Kitsman, atalandira kalata yomuuza kuti akachite nawo sukuluyi, anachita mantha kwambiri. Iye ananena kuti: “Ndinamuuza Yehova nkhawa zanga kuphatikizaponso vuto la kusowa ndalama. Zimenezi zinandipangitsa kuti ndimudalire ndipo sindinanong’oneze bondo. Ndinaona Yehova akundisamalira komanso kundikonda.” Chifukwa cha khama la Mlongo Svitlana, mwamuna wake yemwe si wa Mboni anayamba kupita naye limodzi kumisonkhano yampingo.
Kwa maulendo awiri, apainiya ku Zhytomyr anasamukira kuchipinda cha pansi pa nthaka chifukwa cha phokoso la kulira kwa masayilini ochenjeza anthu. Iwo ankatenthetsa chipindacho pogwiritsa ntchito moto wa nkhuni wa pambaula ndipo anakwanitsa kuchita nawo sukuluyi. Ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto amenewa, Valentyna yemwe anasamukira ku Zhytomyr, ananena kuti: “Sindidzaiwala sukulu imeneyi. Chifukwa ndinkamva ngati ndili pansi pa mapiko a Yehova.”
Mofanana ndi mayiko ena onse, apainiya ku Ukraine anasangalala kwambiri atamva zoti maola a utumiki ofunika kupereka pa mwezi atsitsidwa. Atangomva za chilengezochi, Yulia ananena kuti: “Ndikusangalala kwambiri mumtimamu ndipo chikondi changa pa Yehova chakula. M’mawawu ndinapemphera kwa Yehova ndipo ndinamupempha kuti andithandize kuti ndisasiye kuchita upainiya. Sindinkadziwa kuti andiyankha motani, koma ndinkadziwa kuti andiyankha ndithu. Nditangomva zoti maola a utumiki ofunika kupereka pa mwezi atsitsidwa, ndinayamba kuona kuti ndikufunika kuchita zambiri posonyeza kuyamikira pa zimene amandichitira. Nkhani yosangalatsayi inali ngati keke wokoma kwambiri pambuyo pomaliza sukuluyi.”
Pofika pa 24 January 2023, tinalandira malipoti otsatirawa kuchokera ku Ukraine. Ziwerengerozi zinatsimikiziridwa ndi abale am’dzikolo. Komabe, n’kutheka kuti ziwerengerozi ndi zokwera kwambiri kuposa pamenepa chifukwa sitikutha kulankhulana ndi abale am’zigawo zonse za dzikolo.
Mmene Zakhudzira Abale ndi Alongo Athu
Ofalitsa 47 anafa
Ofalitsa 97 anavulala
Ofalitsa 8,953 anathawa m’nyumba zawo
Nyumba 590 zinawonongekeratu
Nyumba 645 zinawonongeka kwambiri
Nyumba 1,722 zinawonongeka pang’ono
Nyumba za Ufumu 8 zinawonongekeratu
Nyumba za Ufumu 17 zinawonongeka kwambiri
Nyumba za Ufumu 76 zinawonongeka pang’ono
Ntchito Yopereka Chithandizo
Pali Makomiti Othandiza pa Ngozi za Mwadzidzidzi okwana 26 omwe akugwira ntchito ku Ukraine
Nyumba 46 zinakonzedwa
Nyumba za Ufumu 5 zinakonzedwa
Anthu 54,445 anathandizidwa ndi makomitiwa kuti athawire kumalo otetezeka
Ofalitsa 27,655 anathawira kumayiko ena komwe akuthandizidwa ndi Akhristu anzawo