16 MARCH, 2022
UKRAINE
LIPOTI #3 | Abale Akupitiriza Kusonyezana Chikondi pa Nthawi Yankhondo ku Ukraine
Tili ndi chisoni chifukwa cha imfa ya alongo athu awiri amene anaphedwa ndi mabomba mu mzinda wa Mariupol. Panopa, abale ndi alongo oposa 2,000 akulephera kuthawa chifukwa cha kumenyana koopsa komwe kukuchitika mumzindawu. Masiku angapo apitawa, a mboni pafupifupi 150 anakwanitsa kuthawa. Abale a m’Komiti Yothandiza Pangozi Zadzidzidzi pamodzi ndi mabungwe ena opereka chithandizo, anabwerera panjira akupita ku Mariupol, magalimoto awo atayamba kuwomberedwa. Tsiku lina, bomba linaphulika pa Malo a Msonkhano pomwenso pali Nyumba ya Ufumu. Panthawiyo abale ndi alongo pafupifupi 200 anali atabisala m’chipinda chapansi panthaka cha Nyumba ya Ufumuyo. Abale ndi alongowa sanavulale koma magalimoto awo anawonongeka ndipo zimenezi zinachititsa kuti zikhale zovuta kwambiri kuti athawe mu mzindawu.
M’bale wina yemwe ndi mkulu (amene chithunzi chake chili m’munsimu), anakwanitsa kuthawa ku Mariupol ndi banja lake ndipo anafotokoza kuti “Nyumba yathu inawonongeka, sitilinso pantchito komanso manambala a anzathu anasokonekera. Ulendo watsiku limodzi unatitengera masiku 6. Pamene tinkatuluka mu mzindawu, m’mbali mwamsewu munkafuka utsi wamabomba. Abale ndi alongo a m’madera omwe tinkadutsa, ankatithandiza ndi chakudya komanso malo ogona. Tinkaona kuti Yehova yemwe ndi Atate wathu akutisamalira mwachikondi . . . Zimenezi zinatichititsa kuti tizimudalira kwambiri.
Amboni amene akuthawa nkhondo ku Ukraine, akuthawira kumayiko ena a ku Europe. Mwachitsanzo, mtumiki wina wothandiza limodzi ndi mkazi wake komanso ana awo atatu azaka 7, 11 ndi 16, anathawira ku Portugal komwe kuli achibale awo omwenso ndi a Mboni za Yehova. Banjali litadikirira kwa maola 11 kuti lidutse paboda, linayenda mtunda wamakilomita oposa 4,000 kwa masiku 4, kuti likafike kwa achibale awo ndipo anafika misonkhano itangotsala pang’ono kuyamba. Ngakhale kuti salankhula Chipwitikizi, koma akupitirizabe kuchita zinthu zokhudza kulambira komanso kulumikiza misonkhano nthawi zonse kudzera pazipangizo zamakono. Abale ndi alongo amumpingowo amachita chidwi kuona kuti banjali limakhala losangalala ngakhale kuti likukumana ndi mavuto.
Mlongo wina amene anathawira ku Germany limodzi ndi banja lake anafotokoza kuti: “Kuwerenga Baibulo, kuganizira zinthu zabwino komanso chiyembekezo chosangalatsa chomwe tonsefe tili nacho, zimatipatsa mphamvu komanso kutilimbikitsa. . . . Taona dzanja la Yehova likutithandiza komanso kutitsogolera kudzera mwa abale athu. Abalewa anatilandira bwino komanso kutithandiza pomwe tinali ku Ukraine, ku Hungary ngakhalenso pomwe tinafika ku Germany kuno.”
Zikuchita kuonekeratu kuti Yehova akuthandiza abale ndi alongo athu okondedwa a ku Ukraine.—Salimo 145:14.
Pofika pa 16 March 2022, tinalandira malipoti otsatirawa kuchokera ku Ukraine. Ziwerengerozi zinatsimikiziridwa ndi abale a m’dzikoli. Chifukwa choti zikukhala zovuta kulankhulana ndi abale okhala m’zigawo zonse za m’dzikoli, n’kutheka kuti ziwerengerozi zikhoza kukhala zokwera kwambiri kuposa pamenepa:
Mmene Zakhudzira Abale ndi Alongo Athu
Ofalitsa 4 anafa
Ofalitsa 19 anavulala
Ofalitsa 29,789 anathawa m’nyumba zawo n’kupita m’madera ena m’dziko lomwelo
Nyumba 45 zinawonongekeratu
Nyumba 84 zinawonongeka kwambiri
Nyumba 366 zinawonongeka pang’ono
Nyumba za Ufumu 16 zinawonongeka
Ntchito Yopereka Chithandizo
Kunakhazikitsidwa Makomiti Othandiza pa Ngozi Zadzidzidzi okwana 27
Ofalitsa 20,981, anathandizidwa ndi makomitiwa kuti apeze malo otetezeka
Ofalitsa 11,973, anathawira kumayiko ena komwe akuthandizidwa ndi Akhristu anzawo