23 MARCH, 2022
UKRAINE
LIPOTI #4 | Abale Akupitiriza Kusonyezana Chikondi pa Nthawi Yankhondo ku Ukraine
Tikupitiriza kupempherera abale ndi alongo athu omwe ali ku Mariupol komwe asilikali akupitiriza kumenyana komanso kuponya mabomba. N’zomvetsa chisoni kuti abale ndi alongo athu okwana 6 anafa ndi mabomba. Pofika pano, abale ndi alongo omwe afa ku Ukraine akwana 10. Monga mmene zinalembera nyuzipepala zambiri, wiki yathayi asilikali anaphulitsa malo ena oonetsera mafilimu omwe munkabisala anthu opitirira 1,000. Palibe m’bale kapena mlongo aliyense amene anafa pa chiwembuchi, koma abale ndi alongo ochepa anavulala pang’ono.
Abale pafupifupi 750 anathawa ku Mariupol, ndipo enanso pafupifupi 1,600 adakali komweko. Ambiri mwa abalewa akukhala m’chigawo chakum’mawa cha mzindawo chomwe panopo chili m’manja mwa asilikali a Russia.
Monga tinanenera mulipoti lapitalo, abale ndi alongo pafupifupi 200, anabisala m’chipinda chapansi panthaka cha Nyumba ya Ufumu ina yomwe ili pa Malo a Msonkhano. Titakwanitsa kulankhula ndi abale omwe akubisala pamalowa, ananena kuti:
“Pomwe mabomba ankaphulitsidwa, abale ndi alongo ena anali ndi mantha kwambiri moti ena anayamba kulira. Tikamamva kulira kwa mabomba panja, tinkangoti tifa ndi mabombawo kapena ndi moto. Mkulu wina anaganiza zoti tiyambe kuimba nyimbo za Ufumu. Tinaimba nyimbo pafupifupi 10 kapenanso 15. Timati tikaimba nyimbo iyi, timayambanso kuimba ina. Kukamveka chiphokoso chachikulu cha mabomba, makoma achipindacho ankagwezekanso kwambiri. Zikatero, m’pamenenso tinkaimba mwamphamvu kwambiri. Kenako tinawerenga Salimo 27 ndi kukambirana mfundo ya palembalo. Pambuyo pake, aliyense anayamba kutchula lemba la m’Baibulo lomwe amalikonda kwambiri. Akatero amafotokozanso mmene limamulimbikitsira. . . . Tinaonadi kuti Yehova ndi ‘Tate wachifundo chachikulu ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse’ komanso amene angathe kutilimbikitsa pa nthawi yovuta kwambiri.”—2 Akorinto 1:3, 4.
Akulu odzipereka a mu Komiti Yothandiza pa Ngozi Zadzidzidzi, anaika moyo wawo pangozi pogwira ntchito yofufuza abale ndi alongo awo n’kukawapatsa chakudya komanso mankhwala. Nthawi zina abalewa ankayenda chokwawa kuti asilikali asawaombere pomwe akufufuza abale ndi alongo awo. Tikuyamikira kwambiri abale athuwa omwe ‘akuika miyoyo yawo pachiswe’ pofuna kuthandiza Akhristu anzawo.—Aroma 16:4.
Popeza mumzinda wonse mulibe magetsi komanso gasi, alongo olimba mtima akumaphikira panja. Akamaliza, akumapereka chakudyacho kwa ofalitsa omwe ndi achikulire kapena omwe ndi olumala. Pofika pano, ambiri alibenso nyumba, magalimoto komanso katundu. Koma akuyamikira kwambiri kuwasamalira komanso chikondi chomwe Akhristu anzawo akuwasonyeza.
Omwe abisala m’malo osiyanasiyana akuyesetsa kupitirizabe kuchita zinthu zokhudza kulambira monga kuphunzira Baibulo limodzi komanso zikakhala zotheka, akumauzako ena uthenga wa m’Baibulo.
Pofika pa 22 March 2022, tinalandira malipoti otsatirawa kuchokera ku Ukraine. Ziwerengerozi zinatsimikiziridwa ndi abale a m’dzikolo. Komabe n’kutheka kuti ziwerengerozi zikhoza kukhala zokwera kwambiri kuposa pamenepa chifukwa sitikutha kulankhula ndi abale a m’zigawo zonse zadzikolo.
Mmene Zakhudzira Abale ndi Alongo Athu
Ofalitsa 10 anafa
Ofalitsa 27 anavulala
Ofalitsa 33,180 anathawa m’nyumba zawo n’kupita kumadera otetezeka m’dziko lomwelo
Nyumba 78 zinawonongekeratu
Nyumba 102 zinawonongeka kwambiri
Nyumba 484 zinawonongeka pang’ono
Nyumba ya Ufumu imodzi inawonongekeratu
Nyumba za Ufumu 4, zinawonongeka kwambiri
Nyumba za Ufumu 18, zinawonongeka pang’ono
Ntchito Yopereka Chithandizo
Makomiti Othandiza pa Ngozi Zadzidzidzi okwana 27, akugwira ntchito yothandiza anthu
Ofalitsa 25,069 anathandizidwa ndi makomitiwa kuti athawire kumalo otetezeka
Ofalitsa 14,308 anathawira ku mayiko ena komwe akuthandizidwa ndi Akhristu anzawo