13 APRIL, 2022
UKRAINE
LIPOTI #6 | Abale Akupitiriza Kusonyezana Chikondi pa Nthawi Yankhondo ku Ukraine
N’zomvetsa chisoni kuti abale ndi alongo athu ambiri aphedwa pa nkhondo yomwe ikupitirira ku Ukraine. Pofika pano, a Mboni za Yehova okwana 28 afa pa nkhondoyi.
Nyuzipepala zosiyanasiyana zinalemba kuti m’mawiki oyambirira, kumenyana koopsa kunkachitika m’matauni akufupi ndi mzinda kwa Kyiv. Pa ofalitsa pafupifupi 4,900 a m’matauniwa, ofalitsa opitirira 3,500 anathawira kumadera otetezeka.
Zitsanzo zotsatirazi zikusonyeza mmene abale athu okhala m’maderawa akusonyezera kuti ali ndi chikhulupiriro cholimba ngakhale kuti akukumana ndi mayesero aakulu.
Mkulu wina wa m’tawuni ya Makariv dzina lake Oleksandr, anathawira kudera lina lotetezeka m’chigawo chapakati chadziko la Ukraine. Komabe chifukwa chodera nkhawa ofalitsa 4 am’gulu lake la utumiki, omwe zinali zovuta kuwaimbira foni, iye anabwereranso kukawafufuza ngakhale kuti m’deralo munkachitika nkhondo. Iye anafotokoza kuti: “Ndimadziwa kuti atumiki onse a Yehova ndi ofunika kwa mwiniwakeyo. . . . Nditangofika pakhomo la wofalitsa wina, ndinapeza kuti nyumbayo inaphulitsidwa ndi mabomba. Khomo lolowera m’chipinda chapansi linali lotseka ndipo palibe aliyense amene ankayankha ndikamaitana. Zimenezi zinandichititsa mantha kwambiri.” Oleksandr anangophwanya chitsekocho ndipo anapeza gulu la anthu lomwe linkangomuyang’anitsitsa. Anthuwa anali ofalitsa aja limodzi ndi anthu ena okhala nawo pafupi omwe anabisala nawo m’chipindacho.
Wofalitsa wina dzina lake Yaroslav anafotokoza kuti anali atabisala m’chipindamo kwa masiku 8. Iye anati: “Tsiku lililonse, chakudya chathu chinali mabisiketi ndi kapu imodzi yamadzi basi. Koma tinkawerenga Baibulo ndi mabuku athu, kupemphera komanso kulimbikitsana. Nditamva Oleksandr akundiitana, ndinangoti asilikali abwera kudzanditenga. Ndinkangoti basi ndafa. . . . Osadziwa kuti ndi m’bale wabwera kudzatipulumutsa. Tikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa chotipatsa abale ndi alongo omwe amatikonda kwambiri, kutipempherera komanso kulolera kuika moyo wawo pangozi kuti atipulumutse.”
M’bale wina dzina lake Pylyp limodzi ndi m’bale wina, anaganiza zokapereka chakudya kwa abale a m’tawuni ya Borodianka. Pomwe ankapita m’tawuniyi pa 17 March, asilikali analanda galimoto ya Pylyp limodzi ndi zakudya zomwe. Kenako asilikaliwo anamanganso abalewa. Anawamanga ndi unyolo m’manja komanso anawamanga kumaso kuti asamaone n’kukawaika m’kachipinda kena kapansi limodzi ndi amuna ena 7. Patatha masiku awiri, anakawaika muselo ina komwe asilikali ankawamenya usiku. Pylyp anati: “Sindinkadziwa kuti ndikhala ndi moyo. Ndinapemphera kwa Yehova kuti andithandize kuti ndikhalebe wokhulupirika.”
Nthawi ina asilikali akumumenya, Pylyp anayamba kupemphera mokweza. Iye ankapempherera alongo achikulire omwe analibe chakudya, kuti banja lake likhale lotetezeka komanso anathokoza Yehova chifukwa cha zaka zonse zomwe wakhala akumutumikira. Kenako msilikali wolondera anakamubwezera muselo komwe iye anapitiriza kupemphera Iye anapempherera asilikaliwo ndi cholinga choti amvetse kuti iyeyo ndi mnzakeyo sanali anthu oopsa. Kenako abale awiriwa anayamba kulalikira asilikali olondera. Kwa masiku awiri ankalalikira asilikali owalondera omwe ankabwera mosinthanasinthana. Mmodzi wa anthu omwe anagwidwawo, anachita chidwi ndi uthenga wa m’Baibulo ndipo anathokoza kwambiri abalewo. Pa 27 March, abalewa limodzi ndi munthu amene anasonyeza chidwi uja anamasulidwa.
Mlongo wina yemwe amakhala ku Bucha dzina lake Svitlana, analephera kuthawa nkhondo m’dera lawo kwa mawiki awiri. Iye anafotokoza kuti: “Pano m’pamene ndamvetsa kufunika kwa mtendere umene Yehova amatipatsa. Tikakhala ndi mtendere wa Mulungu sizitanthauza kuti nthawi zonse timadziwa zoyenera kuchita. Koma ngakhale pomwe tasoweratu mtengo wogwira, timadalirabe Yehova.”
Pomwe ankathawira kudera lina lotetezeka ku Ukraine komweko, Svitlana analalikira mayi wina ndi wachibale wake. Onse anafika kudera lina komwe analandiridwa ndi banja lina la Mboni. Kutada, banja lija linawapatsa malo ogona. Tsiku lotsatira, mayi uja anapempha kuti akhale nawo pamsonkhano wampingo komanso anapempha Baibulo ndi mabuku athu ena. Mpaka pano, Svitlana amaimbiranabe foni ndi mayiyo.
Pofika pa 12 April 2022, tinalandira malipoti otsatirawa kuchokera ku Ukraine. Ziwerengerozi zinatsimikiziridwa ndi abale a m’dzikolo. Komabe n’kutheka kuti ziwerengerozi ndi zokwera kwambiri kuposa pamenepa chifukwa sitikutha kulankhula ndi abale a m’zigawo zonse za dzikolo.
Mmene Zakhudzira Abale ndi Alongo Athu
Ofalitsa 28 anafa
Ofalitsa 48 anavulala
Ofalitsa 40,778 anathawa m’nyumba zawo n’kupita kumadera otetezeka
Nyumba 278 zinawonongekeratu
Nyumba 268 zinawonongeka kwambiri
Nyumba 746 zinawonongeka pang’ono
Nyumba ya Ufumu imodzi inawonongekeratu
Nyumba za Ufumu 9, zinawonongeka kwambiri
Nyumba za Ufumu 26, zinawonongeka pang’ono
Ntchito Yopereka Chithandizo
Pali Makomiti Othandiza pa Ngozi Zadzidzidzi okwana 27 omwe akugwira ntchito ku Ukraine
Ofalitsa 41,974 anathandizidwa ndi makomitiwa kuti athawire kumalo otetezeka
Ofalitsa 18,097 anathawira kumayiko ena komwe akuthandizidwa ndi Akhristu anzawo