29 APRIL, 2022
UKRAINE
LIPOTI #7 | Abale Akupitiriza Kusonyezana Chikondi pa Nthawi Yankhondo ku Ukraine
Anthu Oposa 210,000 Anapezeka pa Chikumbutso
Ndife osangalala kukudziwitsani kuti Yehova anadalitsa anthu ake omwe ali ku Ukraine moti abale ndi alongo athu m’dziko lonselo, anachita Mwambo Wokumbukira imfa ya Khristu. M’Nyumba za Ufumu zambiri za m’chigawo chakumadzulo kwa Ukraine, komwe abale ndi alongo anabisala atathawa m’nyumba zawo, munachitikira Mwambo wa Chikumbutso. M’madera ambiri, abale anachita Chikumbutsochi m’timagulu ting’onoting’ono. Abale ndi alongo omwe sanakwanitse kuchoka m’nyumba zawo analumikizidwa kudzera pa vidiyokomfelensi.
M’madera ambiri a m’dzikoli, masayilini ochenjeza anthu kuti kukubwera mabomba, anakhala akulira kwa tsiku lonse la Chikumbutso. Koma pomwe kunkada, masayiliniwa anasiya kulira. Sherhiy wa ku Druzhkivka M’chigawo cha Donetsk ananena kuti: “Tinkapemphera kuti Mwambo wa Chikumbutsowu usasokonezedwe ndi mabomba. Mwambowu utangotsala pang’ono kuyamba, sikunamvekenso kuphulika kwa mabomba ndipo masayilini aja sanamvekenso.”
Kagulu ka ofalitsa achikulire ndi enanso athanzi lofooka omwe amakhala ku Nemishaeve kufupi ndi Mzinda wa Kyiv, anali atatha nthawi yoposa mwezi umodzi asanapezeke pamisonkhano yathu. Koma ankapemphera kuti adzapezeke pa Mwambo wa Chikumbutso. Vitaliy amene ndi mkulu, anathandiza ofalitsawa kuti akapezeke nawo pamwambowu. Iye ananena kuti: “Kunalibe magetsi, moti tinagwiritsa ntchito tochi pochita mwambowu. Zipangizo zotenthetsera m’nyumba sizinkagwira ntchito. Tinalibenso zokuzira mawu moti mwana wanga wamkazi ankaimba vayolini kuti tikwanitse kuimba nyimbo.”
Oleksandr yemwe ndi mkulu amene akukhala m’dera lomwe kukuchitika nkhondo, ananena kuti: “Pa nthawi yoitanira anthu Kumwambo wa Chikumbutso, anthu a m’gawo la mpingo wathu sitinawalembere makalata chifukwa anali atathawa nyumba zawo zitaphulitsidwa ndi mabomba. Choncho tinangoitanira anzathu, anthu omwe tinabisala nawo m’zipinda zapansi komanso omwe tinkathawa nawo limodzi.” Ambiri mwa anthuwa m’mbuyomu sankachita chidwi ndi Amboni ndipo ambiri anapezeka pamwambowu.
Ngakhale kuti sitinalandire lipoti lonse la mipingo yonse ya ku Ukraine, tikudziwa kuti anthu opitirira 210,000 anapezeka nawo pamwambowu.
M’bale wina wa ku Ukraine ananena izi pofotokoza mmene anamvera ndi Mwambowu: “Mofanana ndi mmene kuwala kwa moto kumathandizira asodzi usiku kudziwa kuti ayandikira kumtunda, Mwambowu wanditsimikizira kuti tsiku la Yehova latsala pang’ono kufika. Mwambo wachaka chino walimbitsa kwambiri chikhulupiriro changa.”
Pofika pa 21 April 2022, tinalandira malipoti otsatirawa kuchokera ku Ukraine. Ziwerengerozi zinatsimikiziridwa ndi abale a m’dzikolo. Komabe n’kutheka kuti ziwerengerozi ndi zokwera kwambiri kuposa pamenepa chifukwa sitikutha kulankhula ndi abale a m’zigawo zonse za dzikolo.
Mmene Zakhudzira Abale ndi Alongo Athu
Ofalitsa 35 anafa
Ofalitsa 60 anavulala
Ofalitsa 43,792 anathawa m’nyumba zawo n’kupita kumadera otetezeka
Nyumba 374 zinawonongekeratu
Nyumba 347 zinawonongeka kwambiri
Nyumba 874 zinawonongeka pang’ono
Nyumba ya Ufumu imodzi inawonongekeratu
Nyumba za Ufumu 10, zinawonongeka kwambiri
Nyumba za Ufumu 27, zinawonongeka pang’ono
Ntchito Yopereka Chithandizo
Pali Makomiti Othandiza pa Ngozi Zadzidzidzi okwana 27 omwe akugwira ntchito ku Ukraine
Anthu 44,971 anathandizidwa ndi makomitiwa kuti athawire kumalo otetezeka
Ofalitsa 19,961 anathawira kumayiko ena komwe akuthandizidwa ndi Akhristu anzawo