23 MAY, 2022
UKRAINE
LIPOTI #8 | Abale Akupitiriza Kusonyezana Chikondi pa Nthawi Yankhondo ku Ukraine
Abale Akupitiriza Kulimbikitsa Akhristu Anzawo Pomwe Nkhondo Ikupitirira ku Ukraine
Pomwe zinthu zikuipiraipira ku Ukraine, nthambi ya Ukraine ikuchita khama kuchititsa maulendo aubusa kwa abale ndi alongo a m’dzikolo. Abale onse audindo m’dzikolo akugwira ntchito yolimbikitsa ofalitsa masauzande omwe anathawira m’madera osiyanasiyana. Abale ndi alongo akulimbikitsidwa kwambiri ndi maulendowa. Nthawi ina m’bale wa m’Komiti ya Nthambi anayendera abale ndi alongo omwe anathawira m’chigawo chakumadzulo cha dziko la Ukraine. Pambuyo pa ulendowo, mlongo wina amene akukhala m’Nyumba ya Ufumu ina mumzinda wa Uzhgorod limodzi ndi anthu ena pafupifupi 30, anafotokoza kuti: “Ndinamva ngati kuti Yehova wandikumbatira.”
Abale akugwira ntchito mwakhama polimbikitsa abale olimba mtima okwana pafupifupi 100 omwe ali m’Makomiti Othandiza pa Ngozi Zadzidzidzi okwana 27. Ihor, amene ali mu imodzi ya makomitiwa ananena kuti: “Pamene ndinkauzidwa kuti ndiyamba kutumikira m’Komiti Yothandiza pa Ngozi Zadzidzidzi, ine ndi mkazi wanga tinali titathawa kale kwathu ndipo tinkakhala m’nyumba ina. Titatopa, m’bale wa m’Komiti ya Nthambi ngakhale kuti amakhala ndi zochita zambiri, anakwanitsa kudzatiyendera komanso kutimvetsera pomwe tinkafotokoza mmene zinthu zilili. Tinaona kuti ankatidera nkhawa.” Ihor anapitiriza kunena kuti: “Tikakumana ndi vuto linalake ndipo zikuoneka kuti palibenso chomwe tingachite koma kupemphera kwa Yehova basi kuti atitsogolere, timaonadi iye akutithandiza.”
Ponena za Nyumba za Ufumu zomwe zili m’madera omwe mukuchitika nkhondo, Nyumba za Ufumu 4 zinawonongekeratu, 8 zinawonongeka kwambiri ndipo zina zokwana 33 zinawonongeka pang’ono.
Pofika pa 17 May 2022, tinalandira malipoti otsatirawa kuchokera ku Ukraine. Ziwerengerozi zinatsimikiziridwa ndi abale am’dzikolo. Komabe n’kutheka kuti ndi zokwera kwambiri kuposa pamenepa chifukwa sitikutha kulankhulana ndi abale a m’zigawo zonse zadzikolo.
Mmene Zakhudzira Abale ndi Alongo Athu
Ofalitsa 37 anafa
Ofalitsa 74 anavulala
Ofalitsa 45,253 anathawa m’nyumba zawo n’kupita kumadera otetezeka
Nyumba 418 zinawonongekeratu
Nyumba 466 zinawonongeka kwambiri
Nyumba 1,213 zinawonongeka pang’ono
Nyumba za Ufumu 4 zinawonongekeratu
Nyumba za Ufumu 8 zinawonongeka kwambiri
Nyumba za Ufumu 33 zinawonongeka pang’ono
Ntchito Yopereka Chithandizo
Pali Makomiti Othandiza pa Ngozi Zadzidzidzi okwana 27 omwe akugwira ntchito ku Ukraine
Anthu 48,806 anathandizidwa ndi makomitiwa kuti athawire kumalo otetezeka
Ofalitsa 21,786 anathawira kumayiko ena komwe akuthandizidwa ndi Akhristu anzawo