10 JUNE, 2022
UKRAINE
LIPOTI #9 | Abale Akupitiriza Kusonyezana Chikondi pa Nthawi Yankhondo ku Ukraine
Pogwiritsa ntchito Makomiti Othandiza pa Ngozi Zadzidzidzi okwana 27, nthambi ya Ukraine ikupitiriza kuthandiza abale ndi alongo omwe anathawira m’madera osiyanasiyana am’dzikolo. Kuchokera pomwe nkhondo inayamba, zinthu monga chakudya, zovala ndi mankhwala zopitirira matani 250, zakhala zikuitanitsidwa kuchokera m’dziko la Poland. Kuwonjezera pamenepo, chakudya chopitirira matani 80 chinaperekedwa ndi abale omwe akukhala m’madera otetezeka ku Ukraine komweko.
Atalandira chithandizo kuchokera kwa abale a m’Komiti Yothandiza pa Ngozi Zadzidzidzi, mlongo wina wa ku Kyiv dzina lake Valentyna ananena kuti: “Nkhondo itangoyamba, zinali zoopsa kwambiri kupitirizabe kukhala mumzinda wa Kyiv. Choncho ndinathawira kutauni ina yaing’ono yomwe ili m’chigawo cha Cherkasy. Moti ndakhala kuno kwa miyezi yopitirira iwiri tsopano. Abale ndi alongo a mpingo wakuno andithandiza kwambiri. Amandibweretsera makatoni azakudya komanso mankhwala. Ndikaona mmene amandithandizira, zimandikhudza mtima kwambiri. M’katoni ina yomwe ndinalandira, munali khadi komanso chithunzi chomwe anajambula ndi mwana wina wazaka 4 dzina lake Blanca. . . . Ndidzasungabe zinthuzi kuti ndizikumbukira. Ndikuthokoza abale ndi alongo onse ndipo ndikuthokozanso kwambiri Yehova.”
Palinso mlongo wina wolumala wazaka 83 wa ku Sieverodonetsk. Mlongoyu dzina lake ndi Valentyna ndipo ananena kuti: “Pamene nkhondo inkayamba n’kuti ndikukhala ndekha. Mwana wanga wamwamuna anamwalira nkhondo isanayambe. Mabomba ankaphulitsidwa tsiku lonse ndipo zinali zoopsa kwambiri kukhalabe mumzindawo. Kunalibe madzi, magetsi, gasi komanso netiweki inkavuta kwambiri. Ndimathokoza kwambiri abale omwe anaika moyo wawo pangozi kuti andithandize.”
Mlongoyu anapitiriza kunena kuti: “Kenako abale anandisamutsira ku mzinda wa Dnipro komwe ndi kotetezekako limodzi ndi alongo enanso awiri olumala. Ku Dnipro abale anandipezera malo okhala. Panopo ndimakhala ndi banja lina la Akhristu anzanga omwe amandisamalira. Timangokhala ngati anthu a m’banja limodzi. Anandipezeranso foni kuti ndizitha kulumikiza misonkhano komanso kupereka ndemanga. Sindidzaiwala kukoma mtima komwe abale akhala akundisonyeza.”
Ndife osangalala ndiponso tikuthokoza kwambiri Atate wathu wachikondi Yehova, amene akupitirizabe kusamalira abale ndi alongo athu a ku Ukraine kuti ‘asamasowe chilichonse chabwino.’—Salimo 34:10.
Pofika pa 7 June 2022, tinalandira malipoti otsatirawa kuchokera ku Ukraine. Ziwerengerozi zinatsimikiziridwa ndi abale a m’dzikolo. Komabe n’kutheka kuti ziwerengerozi ndi zokwera kwambiri kuposa pamenepa chifukwa sitikutha kulankhulana ndi abale a m’zigawo zonse za dzikolo.
Mmene Zakhudzira Abale ndi Alongo Athu
Ofalitsa 42 anafa
Ofalitsa 82 anavulala
Ofalitsa 46,145 anathawa m’nyumba zawo n’kupita kumadera otetezeka
Nyumba 469 zinawonongekeratu
Nyumba 540 zinawonongeka kwambiri
Nyumba 1,405 zinawonongeka pang’ono
Nyumba za Ufumu 5 zinawonongekeratu
Nyumba za Ufumu 8 zinawonongeka kwambiri
Nyumba za Ufumu 33 zinawonongeka pang’ono
Ntchito Yopereka Chithandizo
Pali Makomiti Othandiza pa Ngozi Zadzidzidzi okwana 27 omwe akugwira ntchito ku Ukraine
Anthu 50,663 anathandizidwa ndi makomitiwa kuti athawire kumalo otetezeka
Ofalitsa 22,995 anathawira kumayiko ena komwe akuthandizidwa ndi Akhristu anzawo