Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

23 JUNE, 2022
UKRAINE

Mmene Ndinayendera Popita Kumalo Otetezeka

Anastasia Khozyainova Akufotokoza Mmene Anapulumukira pa Nkhondo ya ku Ukraine

Mmene Ndinayendera Popita Kumalo Otetezeka

M’mawa wa pa 24 February 2022, ndinadzuka nditamva chiphokoso. Poyamba ndinkaganiza kuti ndi phokoso la mabingu a mvula chifukwa kunkagwa mvula. Koma linali phokoso la mabomba.

Ndinaganiza zothawa n’kusiya nyumba yanga yomwe inali mkatikati mwa mzinda wa Mariupol. Mawa lake, ndinapita kunyumba kwa agogo anga a Iryana omwe ankakhala kunja kwa mzinda wa Mariupol. Kenako kunabweranso mayi anga a Kateryna ndipo tinayamba kukhala anthu 4, ine, mayi anga, agogo ndi khazeni wanga. Kwa kanthawi ndithu tinali otetezeka kunyumba kwa agogo koma masiku ambiri tinkagona m’chipinda chapansi panthaka.

Nthawi ina titabisala m’chipinda chapansi, bomba linagwera m’dimba lathu lamasamba. Kunamveka chiphokoso choopsa. Zitatero ndinapemphera kwa Yehova. Patangotha wiki imodzi, tinaona kuti sitinalinso otetezeka kunyumba kwa agogo. Choncho tinabwereranso kumzinda wa Mariupol kuti tikapeze njira yothawira kwina. Ndinapempha Yehova kuti atiteteze komanso kuti atithandize kutuluka mumzindawo.

Pofika pa 4 March m’mawa, tinali mumzinda wa Mariupol. Koma kunalibe sitima iliyonse yotuluka chifukwa mzindawo unali utazunguliridwa ndi asilikali. Choncho kwa masiku 10, tinakabisala m’malo oonetsera mafilimu limodzi ndi anthu ena ambirimbiri. Kumalowa kunadzaza ndi anthu moti tinkagona pansi. Malowa anali auve komanso zinali zovuta kupeza chakudya ndi madzi otentha. Kuti tipeze zinthu, tinkaima pamzere kwa maola angapo.

Tsiku lina, bomba linaphulikira pafupi kwambiri ndi malo omwe tinabisalawa. Bombalo linali lamphamvu kwambiri moti m’mawindo ambiri magalasi anachoka ndipo chisanu choopsa chinayamba kulowa.

Anastasia ndi mayi ake a Iryna komanso khazeni wake Andrii

Kodi n’chiyani chinandithandiza pa nthawi yovutayi? Inali nkhani ya Yobu. Ndikaona anthu akuchita mantha chifukwa cha kuphulika kwa mabomba, ndinkawerenga nkhani ya Yobu m’Baibulo langa. Ndikatero ndinkamvako bwino. Ndinkamva ngati kuti ndakhala pafupi ndi Yobu ndipo ndikumuuza kuti: “Tsopano ndikumvetsa mmene unkamvera.” Yobu analuza zinthu zake zonse monga: banja lake, thanzi lake komanso chuma chake. Koma ine ndinangoluza katundu yekha. Ndinali ndi anthu a m’banja langa ndipo tonse tinali moyo komanso tinali bwino. Pa nthawiyi m’pamene ndinazindikira kuti zinthu sizinafike poipa kwambiri ngati mmene zinalili ndi Yobu. Nditaganizira zimenezi maganizo anga anakhalako m’malo.

Pa 14 March tinamva kuti gulu lina linakwanitsa kutuluka mumzindawo bwinobwino. Kenako ifenso tinaganiza zotuluka. Limodzi ndi anthu enanso omwe tinali nawo komwe tinabisala kuja, tinapeza magalimoto omwe tinakwera.

Magalimoto 20 anatuluka mumzindawo mondondozana. Anthu tonse 14 omwe tinali pagulu lathu, tinapanikizana kumbuyo kwa galimoto. Tili m’njira tinkaona mabomba akuphulika paliponse ndipo ndinkapemphera pafupipafupi. Titangotuluka mumzinda wa Mariupol, dalaivala wathu anaimitsa galimoto n’kuyamba kulira. Iye anayesetsa kwambiri kuzemba mabomba omwe anatcheredwa mumsewu. Patatha masiku awiri, tinamva kuti malo oonetsera mafilimu omwe tinabisalamo aja aphulitsidwa ndipo anthu pafupifupi 300 aphedwa.

Kenako patatha maola 13 tinafika ku Zaporizhia. Mawa lake m’mawa, tinakwera sitima yopita ku Lviv. Mukachipinda kalikonse kasitimayo komwe nthawi zambiri mumangokwera anthu 4 okha, munakwera anthu 16. Mukachipindamo munkatentha kwambiri. Pafupifupi ulendo wonse, ndinangoimirira m’njira yodutsa anthu kuti ndizikwanitsa kupumako mpweya wabwino. Pa 16 March, tinafika ku Lviv komwe abale ndi alongo athu anatilandira mwansangala. Pambuyo pake kwa masiku okwanira 4, tinkakhala mu Nyumba ya Ufumu. Ndinakhudzidwa kwambiri ndi mmene abale ndi alongo ankatisonyezera chikondi moti mpaka ndinagwetsa misozi. Ndinaona kuti inali mphatso yochokera kwa Yehova.

Pa 19 March, tinaganiza zongotulukiratu m’dziko la Ukraine kupita ku Poland lomwe ndi dziko loyandikana nalo. Kumenekonso ineyo, agogo anga, amayi komanso khazeni wanga tinalandiridwa ndi Amboni anzathu. Anatipatsa chilichonse chomwe tinkafunikira. Aliyense anatisonyeza chikondi.

Ndili ndi zaka 19 zokha koma chifukwa cha zonse zomwe ndinakumana nazozi, ndaphunzira kufunika kolimbikitsa chikhulupiriro pa nthawi imene zinthu zilibwino. Chikhulupiriro ndi chothandiza kuti upulumuke. Zikanakhala kuti sindinkaphunzira pandekha nkhondo isanabwere, zinthu zikanakhala zovuta kwambiri.

Yehova ndi Atate wachikondi. Nthawi zonse ndinkamva ngati kuti wandigwira dzanja langa lamanja ndipo akunditsogolera pa ulendo wonse womwe tinayenda. Sindikudziwa kuti ndingadzakwanitse bwanji kumuthokoza pa zonse zomwe anandichitira.—Yesaya 41:10.