Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Nsanja ya Olonda yakhala ikupezeka m’Chiyukireniya padziko lonse kwa zaka 100 zapitazi

4 JANUARY 2024
UKRAINE

Padutsa Zaka 100 Chiyambireni Kufalitsa Nsanja ya Olonda mu Chiyukireniya

Padutsa Zaka 100 Chiyambireni Kufalitsa Nsanja ya Olonda mu Chiyukireniya

Nsanja ya Olonda ya m’Chiyukireniya yoyambirira yomwe inasindikizidwa mu January 1924

Pofika mu January 2024, padutsa zaka 100 kuchokera pamene magazini ya Nsanja ya Olonda inayamba kufalitsidwa mu Chiyukireniya. Uthenga wabwino unafika ku Ukraine chakumayambiriro kwa chaka cha 1891, ndipo anthu ambiri anamvetsera mwachidwi uthenga wa m’Baibulo. Patapita zaka, anthu ambiri oyankhula Chiyukireniya anayamba kukonda mfundo za m’Baibulo. Komabe, chifukwa choti ku Ukraine kunali mavuto azandale, chitadutsa chaka cha 1900, anthu ambiri oyankhula Chiyukireniya anasamukira m’mayiko ena makamaka ku Canada ndi ku United States.

Mu 1923, M’bale J. F. Rutherford atapita ku Canada, anapempha M’bale Emil Zarysky yemwe makolo ake anachokera ku Ukraine kuti akathandize kumasulira Nsanja ya Olonda mu Chiyukireniya. Emil anali atangoyamba kutumikira monga mpainiya (pa nthawiyo ankatchedwa akopotala) ankatumikiranso monga woyendera dera (pa nthawiyo ankatchedwa kuti woyang’anira woyendayenda). Emil ndi mkazi wake Mariya anali ndi ana 5. Komabe, Emil anavomera pempho la M’bale Rutherford, ndipo Nsanja ya Olonda yoyambirira ya Chiyukireniya inatuluka mu January 1924. Emil anagwira mokhulupirika ntchito yomasulira kwa zaka 40. Mwana wake wamkazi dzina lake Rose, anati: “Chimene ndikukumbukira kwambiri ndi phokoso la mashini omwe bambo anga ankagwiritsa ntchito potayipa, lomwe linkamveka m’nyumba mwathu.”

Mu 1964, Emil anaphunzitsa M’bale Maurice Saranchuk ndi mkazi wake Anne kugwira ntchito yomasulira Nsanja ya Olonda m’Chiyukireniya. Banjali linagwira ntchitoyi mwakhama ndipo nthawi zina ankagwira ntchito yomasulirayi atakhala kumbuyo kwa galimoto yawo pa nthawi yopuma akakhala kuntchito yolembedwa. Patapita nthawi, panakonzedwa dongosolo lakuti azigwiritsa ntchito chipinda chaching’ono ku Nyumba ya Ufumu kuti chikhale ngati ofesi yomasulira mabuku. Mu 1977, banja la a Saranchuk linaitanidwa kuti lizikatumikira ku Beteli ya ku Canada. M’kupita kwa nthawi, abale ena apabeteli omwe ankalankhula Chiyukireniya anaphunzitsidwa kuti azimasulira molondola Nsanja ya Olonda komanso mabuku ena ofotokoza Baibulo.

Kumanzere: Emil ndi Mariya Zarysky, omwe anali oyamba kumasulira magazini ya Nsanja ya Olonda m’Chiyukireniya mu 1924. Kumanja: Maurice ndi Anne Saranchuk omwe anayamba kuthandiza pa ntchito yomasulira Nsanja ya Olonda m’ma 1960

Chakumapeto kwa 1940, ntchito ya Mboni za Yehova ku Soviet Union inaletsedwa. Kwa zaka zambiri zimene ntchito yathu inali yoletsedwa, abale athu anapeza njira zatsopano zotumizira Nsanja ya Olonda ndi mabuku ena a Chiyukireniya ku Ukraine. Mabukuwa akafika ku Soviet Union, abale ankawakopera mosamala ndi kuwagawa kuti abale onse alandire chakudya chauzimu. Kenako ulamuliro wa Soviet Union utatha mu 1991, abale ndi alongo athu ku Ukraine anayambiranso kulambira mwaufulu. Posakhalitsa, gulu la omasulira m’Chiyukireniya linakhazikitsidwa ku ofesi ya nthambi ya Germany. Patapita nthawi, omasulirawa anasamukira ku Poland ndipo anakhala kumeneko mpaka pamene ofesi ya nthambi yatsopano ya Ukraine inamalizidwa mu 2001. Mlongo wina yemwe wakhala akugwira ntchito yomasulira m’Chiyukireniya kwa zaka 30, ananena kuti: “Abale ndi alongo omwe anayamba kumasulira, kukopera ndi kugawira Nsanja ya Olonda anagwira ntchito yotamandika yomwe yathandiza kuti anthu ambiri alowe m’gulu la Yehova masiku ano. Panopa ndikamagwira ntchitoyi, ndimalimbikitsidwa kwambiri ndikamaganizira khama lawo.”

Masiku ano, anthu mamiliyoni ambiri omwe amalankhula Chiyukireniya padziko lonse, amasangalala kuwerenga Nsanja ya Olonda m’chinenero chawo. Panopa m’dzikoli muli magulu 67 olankhula chinenerochi ndiponso muli mipingo 541. Magulu ndi mipingo ya chinenerochi akupezekanso m’mayiko monga Belgium, Britain, Canada, Croatia, Czech Republic, France, Germany, Ireland, Italy, Poland, Slovakia, Spain, Sweden, ndi United States.

Tikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa chothandiza kuti Nsanja ya Olonda izipezeka m’Chiyukireniya kuti anthu ambiri ‘azidalira Mulungu.’​—Salimo 78:7.