Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Liudmyla Mozul ndi Kateryna Rozdorska, amuna awo anafa chifukwa cha nkhondo yomwe ikuchitika ku Ukraine. Iwo akukwanitsa kupirira chifukwa chothandizidwa ndi Yehova komanso Akhristu anzawo

22 APRIL, 2022
UKRAINE

“Usiku Umenewo si Kuti Yehova Anangondigwira Dzanja, Komanso Anandinyamula”

Kuganizira Zomwe Yehova Anatilonjeza Kunalimbikitsa Alongo Amasiye a ku Ukraine

“Usiku Umenewo si Kuti Yehova Anangondigwira Dzanja, Komanso Anandinyamula”

Mlongo Liudmyla Mozul ndi Mlongo Kateryna Rozdorska akupirira mavuto komanso chisoni chomwe ali nacho chifukwa chothandizidwa ndi Yehova. Amuna a alongowa omwe ndi Petro Mozul komanso Dmytro Rozdorskyi ali m’gulu la a Mboni za Yehova omwe anafa chifukwa cha nkhondo ya ku Ukraine. N’zomvetsa chisoni kuti pofika pano, abale ndi alongo athu okwana 34 aphedwa pa nkhondoyi. M’bale ndi Mlongo Mozul anabatizidwa mu 1994 ndipo anakhala limodzi m’banja kwa zaka 43.

Petro ndi Liudmyla Mozul

Mlongo Mozul anafotokoza kuti: “Tsiku lililonse, abale ndi alongo amandiuza mawu olimbikitsa. Nthawi zonse amandiimbira foni. Ndinakhudzidwa kwambiri nthambi ya Ukraine itandilembera kalata yotonthoza mpaka ndinagwetsa misozi.”

Nkhondo ya ku Ukraine inayamba pa 24 February, 2022. M’bale Mozul yemwe ankatumikira ngati mtumiki wothandiza mumpingo wachilankhulo chamanja, anaphewa pa 1 March 2022, pomwe iye ndi banja lake ankathawa mabomba ku Kharkiv.

Tsiku limenelo, m’mwamba monse munali ndege zankhondo zomwe zinkaponya mabomba. Apa n’kuti patatha kale masiku angapo, ndege zikuponya maboma mumzindawu. Patsikuli mabomba atayamba kuphulika, pasanathe maminitsi 30, banjali linangotenga zinthu zochepa n’kuyamba kuthawa. M’bale ndi Mlongo Mozul anali m’galimoto imodzi pomwe mwana wawo Oleksii ndi mkazi wake Maryna, anali m’galimoto ina. Mlongo Mozul anati: “Tili mkatikati mwa ulendo, ndege zinayamba kuponya mabomba ndipo galimoto yathu inayamba kugwedezeka chifukwa cha kuphulika kwa mabombawo.”

M’bale Mozul yemwe anali ndi zaka 67 anavulala kwambiri atakhotetsa galimoto mwadzidzidzi poopa kuti angawombane ndi Oleksii. Kenako M’bale ndi Mlongo Mozul anawatengera kuchipatala komwe M’bale Mozul anakafera. Mlongo Mozul anavulala mwendo komanso pamimba ndi zidutswa zazitsulo zochoka ku mabomba omwe ankaphulikawo. Oleksii ndi Maryna sanavulale pangoziyi. Mlongo Mozul anadziwitsidwa za imfa ya mwamuna wawo patatha masiku atatu atawatulutsa m’chipatala.

Mlongoyu anafotokoza kuti: “Ndikaganizira kwambiri za kukoma mtima kwa Yehova komanso za cholinga chake cham’tsogolo, ndimakhala ndi mtendere wamumtima. Ndine wotsimikiza kuti ndidzakumananso ndi mwamuna wanga m’dziko latsopano. Ndipo ndikuona kuchedwa kuti nthawi yosangalatsayi ifike.”

M’bale ndi Mlongo Rozdorskyi anakhala m’banja kwa zaka 8. Ali kuntchito, m’baleyu anaimbira mkazi wake ndipo mawu omaliza omwe anamuuza anali akuti: “Ndifika kunyumbako posachedwa.”

 

Kateryna ndi Dmytro Rozdorksyi

Patangodutsa maola ochepa tsiku lomwelo pa 8 March 2022, mnzake wakuntchito wa m’baleyu anaimbira foni Mlongo Kateryna Rozdorskyi n’kumuuza kuti mwamuna wake waponda bomba ndipo apita naye kuchipatala. M’bale Rozdorskyi anamwalira patatha maola 5 atachitidwa opaleshoni.

Atauzidwa kuti mwamuna wake wamwalira, Mlongo Rozdorskyi ananena kuti: “Usiku umenewo si kuti Yehova anangondigwira dzanja, komanso anandinyamula. Ndinamva kuti Yehova ali nane pafupi kwambiri.”

M’bale Dmytro Rozdorskyi anali ndi zaka 28 ndipo anabatizidwa mu 2006. Iye ankatumikira ngati mkulu mu mpingo wa m’Chigawo cha Donetsk ku Ukraine.

Patapita nthawi yochepa mwambo wamaliro utachitika, Mlongo Rozdorskyi anayenda ulendo wamaola 12 kupita kudera lotetezeka ku Ukraine komweko. Mlongoyu ananena kuti: “Abale ndi alongo a kuno ku Ukraine komanso a m’mayiko ena akhala akundilimbikitsa kwambiri. Anandithandiza kumva kuti amandikonda kwambiri zomwe zandithandiza kupirira chisoni chomwe ndili nacho.”

Mlongoyu anapitiriza kunena kuti: “Ndimalimbikitsidwanso kwambiri ndikamalalikira. . . .Ndikasokonezeka maganizo, ndimakumbukira mawu a m’Baibulo a pa Afilipi 4:6, 7.”

Tikukhulupirira kuti Yehova apitiriza kuthandiza komanso kutonthoza abale ndi alongo athu omwe aferedwa anthu omwe ankawakonda chifukwa cha nkhondo yomwe ikuchitika ku Ukraine.—Salimo 61:1-3.