Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Abale athu akuzunzidwa kwambiri m’madera ena a ku Donetsk ndi ku Luhansk, komwe ndi kum’mawa kwa Ukraine. Pa 30 May, 2018, akuba anathyola Nyumba ya Ufumu ya m’dera la Luhansk n’kubamo zinthu ndipo kenako anaiwotcha.

OCTOBER 15, 2018
UKRAINE

Chipembedzo cha Mboni za Yehova Chaletsedwa ku “Donetsk People’s Republic”

Chipembedzo cha Mboni za Yehova Chaletsedwa ku “Donetsk People’s Republic”

Pa 26 September, 2018, Khoti Lalikulu Kwambiri ku “Donetsk People’s Republic” (DPR), linagamula kuti chipembedzo cha Mboni za Yehova chimachita zinthu zoopsa ndipo linaletsa ntchito zathu nthawi yomweyo. Pa nthawi yozenga mlanduwu, loya woimira boma pa milandu yemwe anakasumira bungwe lathu komanso khotili sanafunse wa Mboni za Yehova wina aliyense kuti amve mbali yawo. A Mboni za Yehova akuzunzidwa kwambiri m’derali. Ndipo chigamulo choti chipembezo chawo chiletsedwe ndi njira inanso yowazunzira yomwe yagwiritsidwa ntchito posachedwapa.

Cham’katikati mwa 2017, Khoti Lalikulu Kwambiri ku “Donetsk People’s Republic” linanena kuti mabuku athu ena ndi “oopsa.” Zimenezi zinachititsa kuti abale athu omwe amakhala m’madera ena a ku Donetsk ndi ku Luhansk, komwe ndi kum’mawa kwa Ukraine, azikumana ndi mavuto. Mu 2017, apolisi anafunsa mafunso a Mboni oposa 170. Akuluakulu a m’maderawa analandanso Nyumba za Ufumu. Pofika pa 29 August, 2018, Nyumba za Ufumu 16 zinali zitalandidwa.

Ngakhale kuti abale athu m’maderawa akukumana ndi mavuto onsewa, iwo akupitirizabe kudalira “Mulungu wa chipulumutso.”—Salimo 18:46.