Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Panopo a Mboni za Yehova ku Ukraine akhoza kupanga lendi malo kuti achitiremo mapemphero popanda kuletsedwa ndi boma

24 MARCH, 2017
UKRAINE

Khoti Lalikulu ku Ukraine Linalimbikitsa Ufulu Wosonkhana Mwamtendere

Khoti Lalikulu ku Ukraine Linalimbikitsa Ufulu Wosonkhana Mwamtendere

Pa 8 September, 2016, Khoti Lalikulu Loona za Malamulo ku Ukraine linagamula kuti anthu ali ndi ufulu wochita misonkhano mwamtendere popanda kusokonezedwa ndi akuluakulu a boma. Khotili linathetsa mbali ina ya Lamulo la Zipembedzo lomwe linapangidwa mu 1991. Lamuloli linkanena kuti anthu azipembedzo zosiyanasiyana ayenera kutenga chilolezo ku boma ngati akufuna kusonkhana m’malo ochita kupanga lendi. Khotilo linanena kuti zimene lamuloli limanena ndi zosagwirizana ndi ufulu wosonkhana mwamtendere womwe malamulo oyendetsera dzikolo amapereka kwa anthu. A Mboni za Yehova ku Ukraine anasangalala kwambiri ndi chigamulochi, chifukwa ankakumana ndi mavuto akafuna kupanga lendi malo oti achitiremo misonkhano yawo.

Akuluakulu a Boma Anakana Kupereka Chilolezo Chochitira Msonkhano Wachipembedzo

Kungoyambira pamene Lamulo la Zipembedzo linayamba kugwira ntchito, akuluakulu ena a boma omwe amachita zinthu mokondera anayamba kugwiritsa ntchito lamuloli pofuna kuthetsa mgwirizano womwe anthu ena anapanga ndi a Mboni woti apange lendi malo ochitiramo mapemphero awo. Zoterezi zinachita mu 2012 pamene a Mboni za Yehova masauzande ambiri ankayembekezera kuchita msonkhano wamasiku atatu mu mzinda wa Sumy, womwe uli kumpoto chakummawa kwa dziko la Ukraine. A Mboniwo anali atasaina kale m’gwirizano wofuna kupanga lendi sitediyamu ya mumzindawo ndipo ntchito yokonzekera msonkhanowo inayambika. A Mboniwa anadziwitsa akuluakulu a boma za msonkhanowo mogwirizana ndi zimene malamulo oyendetsera dzikolo amanena. Kenako, kutangotsala mwezi umodzi kuti msonkhanowo uyambe, akuluakulu a mzinda wa Sumy ananena kuti kungowadziwitsa za msonkhanowo sikunali kokwanira. Iwo ananena zimenezi potengera zomwe zili mu Lamulo la Zipembedzo. Akuluakulu a mzindawo ananena kuti, a Mboni ankafunika kupempha chilolezo n’cholinga choti agwiritse ntchito sitediyamuyo, koma iwo anakana kupereka chilolezocho.

Ngakhale kuti nthawi inali itatha, a Mboni za Yehova anayenera kuyamba kukonzekera zoti akachitire msonkhanowo pamalo ena mu mzinda wa Kharkiv, womwe uli pa mtunda wa makilomita pafupifupi 200 kuchokera mu mzinda wa Sumy. Kusintha kwa maloku kunachititsa a Mboni oposa 3,500 kuti asinthenso zimene anakonzekera poyamba zokhudza msonkhanowu. Ambiri mwa iwo sanakwanitse kupita ku Kharkiv kukakhala nawo pamsonkhano wofunika kwambiriwu chifukwa cha uchikulire kapena matenda. Ena analephera kupita chifukwa sanakwanitse kupempha kuntchito kwawo kapena chifukwa chakuti analibe ndalama zoyendera. Chaka chotsatira, akuluakulu a mzinda wa Sumy anagwiritsanso ntchito Lamulo la Zipembedzo pokana zoti a Mboni achitire msonkhano wawo pa sitediyamu ya mu mzindawo.

A Illia Kobel, omwe amagwira ntchito pa ofesi ya Mboni za Yehova ku Lviv anati: “Sikuti ndi mumzinda wa Sumy okha kumene misonkhano yathu inaletsedwa. Kwa nthawi zingapo, takhala tikuvutika kuti tipange lendi malo ochitira misonkhano.” Mwachitsanzo, mu March 2012 akuluakulu a mzinda wa Vinnytsia anakana kuti a Mboni achitire msonkhano wawo mu holo ina imene anapanga lendi, ndipo zimenezi zinapangitsa kuti ayambe kusakasaka malo ena nthawi itatha kale. Patadutsa miyezi ingapo, akuluakulu a ku Mohyliv-Podilskyi anakana kupereka chilolezo choti a Mboni achite misonkhano imene amapanga mlungu uliwonse pa malo ena amene anapanga lendi ngakhale kuti anakhala akuchitira misonkhano yawo pamalopo kwa zaka zitatu. Chifukwa chosowa malo abwino oti achitiremo misonkhano yawo, a Mboniwo anakakamizika kukasonkhana m’nyumba za anthu zomwe zinalibenso malo okwanira.

Mu February 2015, akuluakulu oyang’anira chigawo cha Vinnytsia ananena motsindika kuti a Mboni anaphwanya malamulo kwa nthawi zingapo. Iwo ananena kuti a Mboniwo anaphwanya malamulo polephera kutenga chilolezo choti apange lendi malo ochitiramo mapemphero awo. Ananenanso kuti kungowadziwitsa kuti a Mboni ali ndi msonkhano sikunali kokwanira.

A Mboni Anapeza Njira Yoti Boma Lithetse Vuto la Kutsutsana kwa Malamulo

M’zaka zaposachedwapa, a Mboni za Yehova akhala akusonkhana m’malo awo opempherera popanda kuvutitsidwa ndi akuluakulu a boma. Komabe, ikafika nthawi ya misonkhano ikuluikulu, pamafunika kupanga lendi malo aakulu. Malamulo a dziko la Ukraine amavomereza zipembedzo kuti zikhoza kupanga lendi malo ndi kuchita mapemphero awo mwamtendere ngati atawadziwitsiratu akuluakulu a boma za mapempherowo. A Kobel ananenanso kuti: “Lamulo la Zipembedzo ndi limene linkayambitsa mavutowa chifukwa limanena zosiyana ndi zimene malamulo oyendetsera dziko lino amanena. Malamulo oyendetsera dziko lino sanena kuti zipembedzo ziyenera kutenga chilolezo kwa akuluakulu a boma kuti zichite mapemphero awo. Pofuna kuthetsa vutoli, tinakadandaula za nkhaniyi ku ofesi yomva madandaulo a anthu.”

Ntchito ya ofesi yomva madandaulo a anthu ku Ukraine ndi kuonetsetsa kuti munthu wina aliyense m’dzikolo ali ndi ufulu umene umaperekedwa ndi malamulo oyendetsera dzikolo. Pambuyo pounika madandaulo amene a Mboni za Yehova anapereka, mkulu wa ofesi yomva madandaulo a anthu anavomereza kuti Lamulo la Zipembedzo limanena zotsutsana ndi zimene malamulo oyendetsera dzikolo amanena. Malamulo a dzikolo amapatsa anthu ufulu wopanga lendi malo oti achitirepo mapemphero ngati adziwitsa akuluakulu a boma za mapempherowo. Mosiyana ndi zimenezi, Lamulo la Zipembedzo silivomereza anthu kupanga lendi malo ndi cholinga chochita mapemphero, pokhapokha ngati atenga chilolezo kwa akuluakulu a boma kutatsala masiku osachepera 10 kuti mapempherowo achitike.

Pa 26 October, 2015, a ofesi yomva madandaulo a anthu analembera kalata Khoti Lalikulu Loona za Malamulo a Dziko ku Ukraine kulidziwitsa kuti mbali ina ya Lamulo la Zipembedzo imene imatsutsana ndi malamulo oyendetsera dzikolo, ndi yosavomerezeka. Kalatayo inanena kuti nzika zonse za m’dzikolo zili ndi ufulu wosonkhana pamodzi mwamtendere. Pofuna kutsindika za kufunika kwa ufuluwu, kalatayo inati: “Akuluakulu a boma m’madera osiyanasiyana ayenera kupewa kukhazikitsa malamulo awoawo amene amaphwanyira anthu ufulu wosonkhana pamodzi.” Posonyeza kugwirizana ndi zimene a ofesi yomva madandaulo a anthu ananena, a Mboni za Yehova analembera kalata Khoti Lalikulu Loona za Malamulo ku Ukraine yofotokoza mavuto amene ankakumana nawo akafuna kupanga lendi malo kuti achitirepo mapemphero.

Khoti Lalikulu Loona za Malamulo Linathetsa Lamulo Lomwe Linkaphwanyira Anthu Ufulu Wopembedza

Popereka chigamulo chake pa 8 September, 2016, Khoti Lalikulu Loona za Malamulo ku Ukraine linatsindika mfundo yakuti palibe lamulo lomwe liyenera kutsutsana ndi ufulu wosonkhana mwamtendere umene malamulo oyendetsera dzikolo amapereka kwa anthu, ngati anthuwo adziwitsiratu akuluakulu a boma za msonkhano wawo. Khotilo linatchulanso zimene Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Europe, Gawo 9 ndi 11 limanena pa nkhaniyi. Gawo 9 limapereka ufulu wokhala m’chipembedzo, pomwe Gawo 11 limapereka ufulu wosonkhana popanda kusokonezedwa ndi boma pa zifukwa zosamveka. Choncho khotilo linanena kuti Ndime 5 ya Gawo 21 mu Lamulo la Zipembedzo lomwe linapangidwa mu 1991, ndi losagwirizana ndi malamulo oyendetsera dzikolo. Mbaliyi imanena kuti zipembedzo ziyenera kupempha chilolezo kwa akuluakulu a boma zikafuna kupanga lendi malo oti zichitirepo mapemphero.

Nkhani Yosangalatsa

Panopo kupanga lendi malo ochitira mapemphero sikukudaliranso kuti akuluakulu a boma apereke kaye chilolezo, chomwe nthawi zina ankakana kupereka. Mogwirizana ndi zimene malamulo oyendetsera dziko la Ukraine amanena, a Mboni akhoza kupanga lendi malo ochitira mapemphero ngati atadziwitsiratu akuluakulu a boma za mapempherowo, ndipo akuluakulu a bomawo sangawaletse.

Poyankhula m’malo mwa a Mboni oposa 140,000 ku Ukraine, a Kobel anati: “Chigamulo chaposachedwapa chomwe khotili lapereka chalimbikitsa kwambiri ufulu wosonkhana mwamtendere. Tikuyamikira chifukwa sitizikumana ndi vuto lililonse kuchokera kwa akuluakulu a boma tikafuna kupanga lendi malo ochitira mapemphero.”