NOVEMBER 9, 2018
UKRAINE
A Mboni za Yehova Anasonyeza Mtima Wochereza Komanso Mgwirizano pa Msonkhano Wapadera ku Ukraine
A Mboni za Yehova ku Ukraine analandira abale ndi alongo awo masauzande ambiri omwe anakachita nawo msonkhano wapadera omwe unachitikira ku Lviv kuyambira pa 6 mpaka 8 July, 2018. Anthu oposa 3,300 ochokera m’mayiko 9 anapita kumsonkhanowu kuti akapindule ndi pulogalamu yauzimu pamsonkhano wamutu wakuti “Limbani Mtima.” Iwo anasangalalanso chifukwa chocherezedwa ndi abale ndi alongo a ku Ukraine.
Kukonzekera msonkhanowu kunayamba mu April 2017, ndipo kwa miyezi 15 a Mboni a m’dziko la Ukraine anadzipereka pa ntchito yothandiza kukonzekera zochitika zosiyanasiyana za pamsonkhanowo, komanso kusamalira alendo omwe anabwera kumsonkhanowu. Alendowo anasangalala ndi zinthu zosiyanasiyana za ku Ukraine monga nyimbo zomwe zinkaimbidwa, kuvina, komanso zakudya za m’dzikolo. Panakonzedwanso zoti alendowo akaone malo osungirako zinthu zakale, nyumba zikuluzikulu zakale, komanso kukaona mbali ina ya mapiri okongola a Carpathian. Nthawi yapadera kwambiri inali pamene alendowo anali ndi mwayi wolowa muutumiki wakumunda ndi abale ndi alongo a m’dzikolo.
Msonkhanowu unachitikira pasitediyamu ina yayikulu mumzinda wa Lviv, ndipo chiwerengero chachikulu cha osonkhana chinali choposa 25,000. Abale ndi alongo ena anaonera nkhani zina za pamsonkhanowu m’masitediyamu okwana 15 komanso m’Nyumba za Ufumu zambiri m’dziko lonselo. Omwe anaonera nkhanizi analipo 125,000 ndipo anthu 1,420 anabatizidwa.
A Ivan Riher, omwe anayankhula m’malo mwa ofesi ya nthambi ku Ukraine anati: “Tinkayembekezera mwachidwi msonkhano wapaderawu komanso mwayi wolandira abale ndi alongo athu ochokera kumayiko ena. Tinasangalala kuchereza alendo athu ndipo tinamva kuti ndife ogwirizana komanso olimba mtima kwambiri monga banja la padziko lonse.”—Salimo 133:1.
Chiwerengero chachikulu cha anthu osonkhana pasitediyamu ya mumzinda wa Lviv chinali 25,489.
M’modzi mwa anthu achikulire kwambiri pa anthu 1,420 omwe anabatizidwa.
M’modzi mwa achinyamata ambiri omwe anabatizidwa pamsonkhanowu.
Alendo ochokera kumayiko ena ndi ofalitsa a ku Ukraine anagwirira limodzi ntchito yoitanira anthu kumsonkhanowu.
Ofesi ya nthambi inapanga lendi holo ya Lviv Opera House yomwe ili ndi malo aakulu kwambiri kuposa maholo ena onse a mumzinda wa Lviv. Alendo omwe anabwera ku kumsonkhanowu anasangalala ndi zochitika zosiyanasiyana monga kuonera magule komanso kumvetsera nyimbo za ku Ukraine. Nyimbo yomaliza kuimbidwa inali ya mutu wakuti “Dzina Lanu Ndinu Yehova.”
A Mboni a m’dzikolo akuvina gule wa anthu a mtundu wa Romany ku Svirzh Castle.
Pamapeto pa msonkhanowu, abale ndi alongo ananyamula zikwangwani zosonyeza kuti amakonda abale ndi alongo omwe anachokera kumayiko ena.