Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

UKRAINE

Mfundo Zachidule Zokhudza a Mboni ku Ukraine

Mfundo Zachidule Zokhudza a Mboni ku Ukraine

A Mboni za Yehova akhala akupezeka ku Ukraine kwa zaka zoposa 100. Dziko la Ukraine litangotsala pang’ono kukhala lodziimira palokha, a Mboni analembetsa ku boma monga chipembedzo chovomerezeka pa 28 February, 1991.

Pa nthawi ya ulamuliro wa Nazi komanso Soviet, a Mboni za Yehova ankachitidwa nkhanza kwambiri ku Ukraine. Pa 8 April, 1951, akuluakulu a boma la Soviet anathamangitsa a Mboni oposa 6,100 kuchoka kumadzulo kwa dziko la Ukraine n’kuwatumiza ku Siberia. Kenako zinthu zinasintha pang’ono mu June, 1965 pamene Khoti Lalikulu Kwambiri ku Ukraine linagamula kuti mabuku a Mboni za Yehova si otsutsana ndi boma la Soviet koma ndi achipembedzo. Akuluakuluwa anasiya kumanga anthu omwe ankawerenga mabuku a Mboni koma anapitirizabe kumanga a Mboni chifukwa chouza ena zimene amakhulupirira. Mu September, 1965, boma linakhululukira a Mboni onse omwe anawatumiza ku Siberia mu 1951 koma ambiri mwa a Mboniwa sanawalole kubwerera komwe ankakhala poyamba. Abale ankazunzidwabe kwambiri mpaka chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1980.

Panopa a Mboni za Yehova akusangalala kuti amasonkhana pamodzi polambira Mulungu mwaufulu komanso ali ndi ufulu wolalikira poyera popanda kuletsedwa ndi akuluakulu a boma. Komabe, anthu omwe amadana ndi a Mboni akhala akuwachitira zankhanza. Akuluakulu a boma sanachite zambiri pothandiza a Mboni kuti asachitidwe nkhanza komanso poteteza nyumba zomwe ankachitiramo misonkhano kuti zisaonongedwe ndipo nthawi zambiri anthu omwe ankachita zimenezi sankawaimba milandu. Anthu ochita zankhanzawa anapezerapo mpata chifukwa choti akuluakuluwa sanachitepo kanthu. Chinanso n’chakuti kum’mawa kwa dziko la Ukraine kunkachitika zachipolowe ndipo zimenezi zinachititsa kuti a Mboni azunzidwe kwambiri.