Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

NOVEMBER 11, 2014
UKRAINE

A Mboni za Yehova Anachita Msonkhano Mwamtendere ku Ukraine Ngakhale Kuti Kuli Nkhondo

A Mboni za Yehova Anachita Msonkhano Mwamtendere ku Ukraine Ngakhale Kuti Kuli Nkhondo

A Anthony Morris a m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova akutulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lomwe lakonzedwanso.

LVIV, Ukraine—Ngakhale kuti nkhondo yavuta kum’mawa kwa dziko la Ukraine, a Mboni za Yehova anachita msonkhano ku Lviv kuyambira pa July 4 mpaka 6 2014. Msonkhanowu unali ndi mutu wakuti “Pitirizani Kufunafuna Ufumu wa Mulungu Choyamba.” Pa msonkhanowu, a Anthony Morris a m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lokonzedwanso lomwe linamasuliridwa m’Chiyukireniya chamakono.

Ofesi ya Mboni za Yehova ya m’dzikoli inakonza zoti mbali zikuluzikulu za msonkhanowu zilumikizidwe patelefoni ndi pa TV m’mizinda 8 komanso m’malo ena 62 a m’dera la Donetsk kumene nkhondo yakula kwambiri. Anthu amene anamvetsera msonkhanowu m’malo onse anakwana 82,832 ndipo pa anthu amenewa, 18,336 anachitira msonkhanowu kusitediyamu ya ku Lviv. Anthu amene anabatizidwa m’malo onsewa anakwana 1,068.

Anthu okwana 18,336 anachita msonkhano wamutu wakuti “Pitirizani Kufunafuna Ufumu wa Mulungu Choyamba” ku Arena Lviv.

Tsiku loyamba msonkhano unasokonezeka chifukwa anthu ena anaopseza kuti musitediyamumo mwaikidwa bomba. Nthawi yomweyo anthu anayamba kutulukamo moti mmene pamatha maminitsi 11, anthu oposa 16,000 omwe anali m’sitediyamuyi anali atatuluka. Kenako akuluakulu a ku sitediyamuyi ananena kuti zoti m’sitediyamumo muli bomba ndi zabodza. Nthawi yomweyo msonkhanowu unayambiranso.

A Vasyl Kobel, omwe amalankhula moimira Mboni za Yehova ku Ukraine, ananena kuti: “Tinasangalala kulandira alendo ambiri kumsonkhanowu. Chinthu chosaiwalika pa msonkhano umenewu ndi kutuluka kwa Baibulo la Dziko Latsopano m’Chiyukireniya, lomwe linakonzedwanso ndipo linatuluka koyamba m’Chingelezi mu October 2013. Timasangalala kwambiri kuuza anzathu zimene Baibulo limalonjeza kuti mtsogolomu tizidzakhala mwamtendere. Zimenezi n’zofunika kwambiri m’dziko lathu makamaka pa nthawi ino pomwe m’dzikoli muli nkhondo.”

Kuchokera M’mayiko Ena:

Lankhulani ndi: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Ukraine: Vasyl Kobel, tel. +38 032 240 9323