Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JUNE 8, 2015
UKRAINE

Makhoti a ku Ukraine Avomereza Kuti Munthu Ali ndi Ufulu Wokana Kulowa Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira

Makhoti a ku Ukraine Avomereza Kuti Munthu Ali ndi Ufulu Wokana Kulowa Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira

Mu 2014, kumadera ena a kum’mawa kwa dziko la Ukraine kunayambika zipolowe komanso nkhondo ndipo pulezidenti analengeza kuti pakufunika kuti anthu ambiri alowe usilikali. Vitaliy Shalaiko, yemwe kale anali msilikali koma panopa ndi wa Mboni za Yehova, anaitanidwa kuti alowenso usilikali. Atakaonekera pamaso pa akuluakulu a asilikali, iye ananena kuti sangalowe usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira koma akhoza kugwira ntchito zina zosakhudzana ndi usilikaliwo.

Akuluakulu a asilikali sanavomereze zimene Shalaiko anapempha mogwirizana ndi ufulu wake ndipo anamuimba mlandu wozemba usilikali pa nthawi imene pankafunika asilikali ambiri. Pa nthawi ya nkhondoyi, Shalaiko anali munthu woyamba m’dzikoli kuimbidwa mlandu chifukwa chokana usilikali potsatira zimene amakhulupirira.

Popeza kuti kale anali msilikali, Shalaiko amadziwa kuti boma limafunitsitsa kuteteza ulamuliro wake ndiponso anthu ake. Komabe iye ankafuna kutsatira mfundo ya m’Baibulo yakuti “perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu, kwa Mulungu.” a Monga Mkhristu ankaona kuti nthawi zonse ayenera kulemekeza moyo komanso kusonyeza chikondi kwa anthu onse. b

Kukhoti Loyamba: Kodi Munthu Akasankha Kugwira Ntchito Zosakhudzana ndi Usilikali Ndiye Kuti Wazemba Usilikali?

Pa 13 November 2014, khoti lina la m’dzikoli linaweruza mlandu wa Shalaiko womwe ankamuganizira kuti anazemba usilikali. Khotili linaona kuti iye sanazembe chifukwa anakaonekera pamaso pa akuluakulu a asilikali. Linagamula kuti Shalaiko “ali ndi ufulu wokana usilikali n’kusankha kugwira ntchito zina zosakhudzana ndi usilikaliwo ngati chipembedzo chake chimaletsa munthu kuti azigwiritsa ntchito zida zankhondo.” Linanenanso kuti “akhoza kuchita zimenezi ngakhale pa nthawi imene pakufunika asilikali ambiri.”

Kuwonjezera pamenepa, khotili linanena kuti ufulu wa Shalaiko ndi “wovomerezeka ndi malamulo a dziko la Ukraine.” Linanenanso kuti Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Ulaya c ndiponso Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya limateteza ufulu wa chipembedzo. Choncho woweruza anagamula kuti Shalaiko alibe mlandu wozemba usilikali. Koma loya woimira boma sanagwirizane ndi chigamulochi moti anachita apilo.

Kukhoti la Apilo: Kodi N’zothekabe Kukana Usilikali pa Nthawi Imene Boma Likufuna Asilikali Ambiri?

Pa nthawi yochita apilo, loya woimira boma ananena kuti malamulo a dziko la Ukraine amasonyeza kuti aliyense ali ndi udindo woteteza dzikolo ndipo udindo umenewu ndi waukulu kuposa ufulu wa chipembedzo kapena wosankha kugwira ntchito zina zosakhudzana ndi usilikali. Iye ananena kuti zimene Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linagamula sizingagwire ntchito pa nthawi imene dziko likufuna asilikali ambiri.

Pa 26 February 2015, khoti la apilo linagamula kuti “munthu akakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira sikuti wazemba usilikali popanda zifukwa zomveka.” Khotili linanenanso kuti mogwirizana ndi zimene Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linagamula, zimene Shalaiko amakhulupirira “n’zofunika kulemekezedwa chifukwa cha zimene zili mu Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Ulaya.” d Panganoli limanena kuti anthu ali ndi ufulu wonena maganizo awo, wotsatira zimene amakhulupirira ndiponso wa chipembedzo.

Khoti la apiloli linanenanso kuti Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Ulaya sililola kuti ‘kudera nkhawa za chitetezo cha dziko kuchititse kuti munthu asapatsidwe ufulu wake.’ Choncho oweruza ananena kuti “boma silingachotse ufulu wa munthu wotsatira zimene amakhulupirira chifukwa chofuna kuteteza dziko.” Iwo anagamulanso kuti malamulo a dziko la Ukraine okhudza ufulu wosankha kugwira ntchito zina zosakhudzana ndi usilikali amagwiranso ntchito ngakhale pa nthawi imene pakufunika asilikali ambiri. Khoti la apilo linagwirizana ndi zimene khoti loyamba lija linagamula zoti Vitaliy Shalaiko alibe mlandu.

Si Mlandu Kuchita Zinthu Mogwirizana ndi Ufulu Wako

Zimene makhotiwa anagamula zikutsimikizira kuti munthu ali ndi ufulu wokana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira ndiponso wosankha kugwira ntchito zina zosakhudzana ndi usilikaliwo ngakhale pa nthawi ya nkhondo. Zimene anagamula pa mlandu wa Shalaiko zimagwirizana ndi malamulo a m’mayiko ambiri okhudza kulemekeza ufulu wa munthu wotsatira zimene amakhulupirira. e

Komabe loya woimira boma anachitanso apilo kukhoti lalikulu la m’dzikoli ndipo anafotokoza zifukwa zomwe zija zimene khoti la apilo linalo linagamula kuti si zomveka. Pa 30 April 2015, maloya a Shalaiko analemba kalata yotsutsa apiloyo.

Vitaliy Shalaiko ndi mmodzi wa a Mboni ambiri a ku Ukraine omwe amaitanidwa kuti alowe usilikali. Iwo amakaonekera kwa akuluakulu a asilikali ndipo amapempha mwaulemu kuti agwire ntchito zina zosakhudzana ndi usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Nthawi zambiri boma limalemekeza zimene a Mboniwo amapempha ndipo ndi ochepa amene amaimbidwa mlandu. Panopa khoti lalikulu la ku Ukraine ndi limene lili ndi udindo wosankha kuti ufulu wa a Mboni wokana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira uzilemekezedwa nthawi zonse.

b Werengani nkhani yakuti, “N’chifukwa Chiyani Simupita Kunkhondo?

c Mu 1997, dziko la Ukraine linavomereza Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Ulaya.

d Khoti la apilo lija linayendera zimene Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linagamula pa mlandu wa pakati pa boma la Russia ndi a Mboni za Yehova a ku Moscow limodzi ndi ena komanso mlandu wa pakati pa Bayatyan ndi boma la Armenia.

e Onani mlandu wa pakati pa Bayatyan ndi boma la Armenia [GC], na. 23459/03, §§ 98-111, ECHR 2011; wa pakati pa Jeong et al. ndi boma la Republic of Korea, UN Doc CCPR/C/101D/1642-1741/2007 (24 March 2011) §§ 7.2-7.4.