Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Nyumba yotchedwa The Royal Courts of Justice yomwe muli Khoti Lalikulu komanso Khoti la Apilo la ku England ndi ku Wales

MAY 12, 2020
UNITED KINGDOM

Khoti la ku England Lagamula Motikomera pa Nkhani ya Amene Ali Woyenerera Kukhala m’Gulu Lathu

Khoti la ku England Lagamula Motikomera pa Nkhani ya Amene Ali Woyenerera Kukhala m’Gulu Lathu

Pa 17 March, 2020, Khoti la Apilo ku England ndi ku Wales linagamula kuti a Mboni za Yehova ali ndi ufulu woyendera malangizo a m’Baibulo okhudza dongosolo lochotsa munthu mumpingo. Khotili linanena kuti palibe chifukwa choti lisinthe zimene Khoti Lalikulu linagamula pankhaniyi.

Pofotokoza za chigamulo chake, Khoti Lalikulu linanena kuti mpingo uli ndi ufulu wolengeza kuti munthu wina salinso wa Mboni za Yehova ndipo sikuti umalengeza zimenezi ndi cholinga chofuna kuipitsa mbiri ya munthuyo. Popereka chigamulochi, woweruza milandu wa khotili, dzina lake Richard Spearman, anati: “Gulu lachipembedzo limene limayesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo lili ndi mphamvu zochotsa munthu wochimwa mumpingo ndipo kuchita zimenezi kulibe vuto lililonse. Kuchita zimenezi n’kofunika chifukwa munthu yemwe walephera kapena sakufuna kutsatira mfundo za m’Baibuloyo, amasonyeza kuti sali woyenerera kukhala m’gulu la chipembedzo limenelo. Ndipotu ngati munthuyo sanachotsedwe mumpingo akhoza kusokoneza makhalidwe a anthu ena mumpingomo.”

Khotili litapereka chigamulo chimenechi, munthu yemwe anakadandaula za nkhaniyi anakapanga apilo ku Khoti la Apilo. Koma Khoti la Apilo linakana pempholo ndipo linanena kuti “pempholo ndi losamveka.” Linanenanso kuti zimene Khoti Lalikulu linagamula “n’zolondola” ndipo “mpingo unagwiritsa ntchito mphamvu zake moyenera pochotsa munthuyo mumpingo.”

A Shane Brady omwe ndi loya wa Mboni za Yehova anati: “Chigamulochi ndi chogwirizana ndi zigamulo zingapo za makhoti a ku England, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe, komanso makhoti a apilo ku Canada, Continental Europe, ndi ku United States. Zigamulo zonsezi zikutsimikizira mfundo yoti a Mboni za Yehova ali ndi ufulu wosankha anthu omwe ndi oyenera kukhala m’gulu lawo.”

Ndife osangalala kuti Khotili linagwirizana ndi zoti tili ndi ufulu womvera zimene Baibulo limanena komanso woteteza mipingo yathu kuti isasokonezedwe ndi makhalidwe oipa.—1 Akorinto 5:11; 2 Yohane 9-11.