Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

5 SEPTEMBER, 2017
UNITED KINGDOM

A Mboni Anapatsidwa Mphotho Yapamwamba Chifukwa Chogwiritsa Ntchito Njira Zamakono Pomanga Nthambi Yawo Yatsopano ku Britain

A Mboni Anapatsidwa Mphotho Yapamwamba Chifukwa Chogwiritsa Ntchito Njira Zamakono Pomanga Nthambi Yawo Yatsopano ku Britain

LONDON—A Mboni za Yehova akumanga maofesi awo atsopano ku Britain ndipo akatswiri avomereza mapulani komanso njira zomwe zikutsatiridwa pomanga maofesiwa. Akatswiri a bungwe lina la sayansi komanso loona za zomangamanga anaona kuti mapulani ndiponso njira zimene a Mboni akugwiritsa ntchito ndi zapamwamba kwambiri. Maofesiwa ali mumzinda wa Chelmsford m’chigawo cha Essex komwe ndi chakum’mawa kwa London ndipo pali mtunda wa makilomita 70 kuchoka ku London. Maofesiwa ndi achiwiri kulandira mphotho yapamwamba kuchokera ku bungweli.

Pa 25 May 2017, a Mboni za Yehova analandira mphoto yapamwamba kwambiri chifukwa chomanga ma ofesi awo a ku Chelmsford mwapamwamba kwambiri.

Bungweli limapereka mphotho likaona mapulani a kamangidwe komanso likaona kuti zinthu zotsatirazi zili bwino: kuchuluka kwa mphamvu zamagetsi zogwiritsidwa ntchito, thanzi la anthu, kagwiritsidwe ntchito ka malo ndi kasamaliridwe kake, zipangizo zomangira, kuteteza chilengedwe, katayidwe ka zinyalala, kusamalira madzi komanso kayendedwe ka anthu pofika komanso kuchoka pamalo ogwirira ntchito. Mphotho zomwe bungweli limapereka zili m’magulu 5 ndipo zimayamba ndi mphotho yaing’ono kumalizira ndi yaikulu kwambiri. Kuti a Mboni apatsidwe chilolezo chomanga maofesiwa, Khonsolo ya Mumzinda wa Chelmsford inafuna kuti a Mboniwa atsatire njira za kamangidwe ka m’gulu lachitatu. Neil Jordan ndi mkulu woona za mapulani ku Khonsolo ya Mumzinda wa Chelmsford. A Jordan anati: “Tasangalala kwambiri kuti mapulani a Mboni za Yehova ndi ogwirizana ndi zimene timafuna ndipo aposanso ndondomeko zomwe Khonsolo yathu imafuna.” A Jordan ananenanso kuti: “Maofesi a Mboniwa akhala ochititsa chidwi kwambiri mumzindawu ndipo akhala chitsanzo chabwino kwambiri pa kamangidwe kovomerezeka.”

Chochititsanso chidwi kwambiri kuwonjezera pa mphotho yaikulu kwambiri yomwe a Mboniwa anapatsidwa, asonyezanso kuti ali ndi cholinga choteteza chilengedwe. Njira zomwe a Mboniwa anakhazikitsa zikuthandiza kuchepetsa mpweya wa kaboni ndi matani 2, 480. Mpweyawu umatha kuchokera ku utsi wa magalimoto komanso zinthu zina. Pofuna kuchepetsa kuchuluka kwa mpweyawu, a Mboniwa anakonza zoti ogwira ntchito ena azigonera pomwepo pomwe ena amakawasiya m’makwawo pa maminibasi ndi njira zina za mayendedwe m’malo moti aliyense aziyendetsa galimoto yake zomwe zikanachititsa kuti pazikhala mpweya wochuluka wa kaboni. Zimenezi zachititsa kuti a Mboni apatsidwe mphotho ina yomwe n’koyamba kuperekedwa. A Jordan ananenanso kuti “ntchitoyi yathandiza kuti titulukirenso njira ina yochepetsera mpweya woipawu. Komanso zithandiza bungwe lathu kuyamba kutsatira njira zina zomwe timalephera kuzikwaniritsa.”

A Pallab Chatterjee ndi mkulu woonetsetsa kuti a zomangamanga akutsatira njira zoteteza chilengedwe.

A Pallab Chatterjee ndi mkulu woonetsetsa kuti a zomangamanga akutsatira njira zoteteza chilengedwe. A Chatterjee anagwira ntchito limodzi ndi a Mboni za Yehova pamalowa. Iwo anafotokoza zomwe anaona poyerekeza ndi ntchito za mtunduwu zomwe anagwirapo ndi anthu ena. Iwo ananena kuti: “Ndaona zachilendo pamalowa. Anthu ake ndi aubwenzi komanso ogwirizana. Zimenezi sizichitikachitika. Komanso a Mboniwa ayesetsa kutsatira mapulani ndi njira zambiri za kamangidwe mogwirizana ndi ndondomeko za bungwe lathu. Ndipo sikuti maganizo awo anali ongofuna kutsatira zomwe tinagwirizana koma kuyambira pachiyambi pomwe anali ndi cholinga chomanga maofesi apamwamba komanso amakono pogwiritsa ntchito njira zoteteza chilengedwe. Chandisangalatsanso ndi chakuti anayesetsanso kumva maganizo a anthu osiyanasiyana omwe akukhala m’dera lino komanso a ena omwe akuyembekezeka kudzakhala kuno. Pa ntchito zonse zomwe ndagwirapo, ntchitoyi inali yosangalatsa kwambiri.”

A Andrew Schofield ndi mneneri wa Mboni za Yehova ku Britain. Iwo ananena kuti: “Kwa zaka pafupifupi 60 maofesi athu a kuno ku Britain anali ku London. Koma chifukwa chakuti pali anthu ambiri omwe akufuna mabuku athu ndi zinthu zina, tinafunikanso kupeza malo aakulu ogwirira ntchito. Tinayamba kukonza malo ano mu April, 2015 ndipo ndi aakulu mahekitala 34. Tikuyembekezera kudzamaliza ntchito yomangayi kumapeto kwa 2019.”

Lankhulani ndi:

Kuchokera Kumayiko Ena: David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000

United Kingdom: Andrew Schofield, +44-20-8906-2211