28 APRIL, 2021
UNITED STATES
Anthu Athawa Kwawo Chifukwa cha Kuphulika kwa Phiri ku Caribbean
Malo
Madera ena a St. Vincent ndi Barbados
Ngozi
Pa 9 April, 2021, kunachitika ngozi yophulika phiri (La Soufrière volcano) ndipo kunatuluka phulusa ndi utsi
Phulusali linachititsa kuti nyumba zigwe, magetsi azime komanso madzi asowe
Zikuoneka kuti ngoziyi ipitirira mwina kwa milungu ingapo
M’mene zakhudzira abale athu
Ofalitsa 185 a ku St. Vincent ndi ku Barbados achoka kwawo
Katundu amene wawonongeka
Panopa n’zosatheka kufika kumalo amene akhudzidwa kwambiri ndi ngoziyi ku St. Vincent moti sitikudziwa mmene katundu wawonongekera
Kupereka thandizo
Abale ndi alongo amene achoka kwawo akulandiridwa ndi a Mboni anzawo m’madera otetezeka ku St. Vincent ndi ku zilumba zina uku akutsatira malangizo odzitetezera ku COVID-19
Komiti yopereka chithandizo (DRC) kwa okhudzidwa ndi COVID-19 inapemphedwa kuti ithandize anthu amene akhudzidwa. Komitiyi ikugwira ntchito limodzi ndi woyang’anira dera komanso akulu popereka madzi akumwa ndi zinthu zina kwa anthu amene akhudzidwa
Nawonso akuluakulu a boma ku St. Vincent ndi ku St. Lucia athandizanso anthu okhudzidwa
M’bale wina wachikulire yemwenso saona ndipo amakhala yekha kudera lomwe lakhudzidwa kwambiri anapulumutsidwa ndi gulu lina la abale ngoziyi itangotsala pang’ono kuchitika. Ali m’galimoto kupita kumalo otetezeka anaona mumsewu muli chipwirikiti chifukwa cha anthu othawa. Mwamwayi ofalitsa onse anapulumutsidwa n’kukafika kumalo otetezeka.
Tikusangalala kuti abale ndi alongo akuthandizidwa, apeza malo ogona komanso akulimbikitsidwa ndipo izi zikuchitika chifukwa choti timatsanzira Mulungu wathu amene ndi “thandizo lopezeka mosavuta pa nthawi ya masautso.”—Salimo 46:1-3.