APRIL 16, 2019
UNITED STATES
Madzi Osefukira Aononga Kwambiri M’chigawo Chapakati ku United States
Mvula yamphamvu kwambiri ndiponso sinowo yemwe anasungunuka zinapangitsa kuti madzi asefukire chapakati pa mwezi wa March 2019 ku Nebraska ndi ku Iowa. Mitsinje m’maderawa inasefukira kwambiri kuposa mmene yakhala ikusefukirira m’mbuyomu, ndipo nawonso madamu anasefukira zomwe zinachititsa kuti nyumba zambiri zionongeke komanso anthu osachepera 4 anafa.
Ofesi ya nthambi ya ku United States yanena kuti pa ofalitsa 5,123 omwe ali m’maderawa, palibe yemwe wafa kapena kuvulala. Komabe, ofalitsa 84 anathawa m’nyumba zawo. Kuonjezera pamenepo, nyumba 8 za abale zinaonongeka kwambiri komanso zina 34 zinaonongeka pang’ono.
Abale ndi alongo ongodzipereka ochokera m’mipingo yapafupi ayamba kale ntchito yoyeretsa limodzi ndi abale a m’Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga. Oyang’anira madera a m’madera omwe akhudzidwa akuthandiza pa ntchito yotonthoza komanso kulimbikitsa abale ndi alongo omwe akhudzidwa ndi kusefukira kwa madziku.
Tikupemphera kuti abale athu apitirize kutonthozedwa ndi thandizo limene akulandira kuchokera kwa abale komanso kulimbikitsidwa ndi mfundo za m’Baibulo pa nthawi yovutayi.—2 Akorinto 1:3, 4.