Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MARCH 28, 2014
UNITED STATES

Matope Oopsa Awononga Zinthu ku Washington

Matope Oopsa Awononga Zinthu ku Washington

Pa March 22, 2014, matope oopsa anakwirira nyumba zambirimbiri ku Snohomish County, Washington, m’dziko la USA. Akuluakulu a m’deralo ananena kuti anthu pafupifupi 90 akusowabe mpaka pano ndipo zatsimikizirika kuti anthu omwe afa ndi 17. Ofesi ya Mboni za Yehova ku United States yanena kuti mzimayi mmodzi wa Mboni ali m’gulu la anthu amene akusowa. Banja lina la Mboni za Yehova linakhudzidwa kwambiri ndi ngoziyo chifukwa mwana wawo wamkazi komanso mdzukulu wawo anafa pangoziyo. Anthu enanso awiri a Mboni anasamuka m’nyumba zawo, ndipo nyumba inanso ya wa Mboni inawonongekeratu. Akulu a m’mipingo ya Mboni m’derali akuthandiza komanso kulimbikitsa anthu amene akukhudzidwa ndi ngoziyi.

Lankhulani Ndi:

Kuchokera Kumayiko Ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000