SEPTEMBER 17, 2020
UNITED STATES
Moto Ukupitirira Kuwononga Zinthu Kumadzulo kwa United States
Malo
California, Oregon ndi Washington
Ngozi yake
Moto wolusa womwe ukufalikira mofulumira kwambiri wawononga malo okwana mahekitala oposa 2 miliyoni kuchokera ku California mpaka ku Washington
Motowu wachititsa kuti anthu azipuma mpweya wowonongeka
Moto umene wawononga ku California waposa moto wina wonse womwe wakhala ukuyaka kumeneko m’mbuyo monsemu
Mmene motowu wakhudzira abale ndi alongo athu
Ofalitsa 4,546 asamuka m’nyumba zawo
Katundu amene wawonongeka
Nyumba 61 zapseratu
Nyumba 16 zawonongeka
Ntchito yothandiza anthu
Makomiti Othandiza pa Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi akupitirizabe kugwira ntchito limodzi ndi oyang’anira madera komanso akulu a m’mipingo pothandiza abale ndi alongo amene asamuka m’nyumba zawo, kwinaku akutsatira malangizo opewera matenda a COVID-19
Ofalitsa omwe akhudzidwa ndi motowu akuyamikira kwambiri zimene Yehova wachita powathandiza kudzera m’gulu lake. Mlongo wina amene nyumba yake inapsa ananena kuti abale anali “ofunitsitsa kutichitira china chilichonse chimene tinkafunikira, ifeyo tisanadziwe n’komwe kuti tikufunikira zimenezo.”
Ngakhale kuti abale ndi alongo amene akhudzidwa ndi motowu akuvutikabe, iwo akuona kuti Yehova akupitiriza kuwasamalira mwachifundo.—Yakobo 5:11.