Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Chithunzi chosonyeza moto wotchedwa Dixie Fire, usiku ku California, U.S.A.

AUGUST 16, 2021
UNITED STATES

Moto Wolusa Ukupitirizabe Kuwononga ku California

Moto Wolusa Ukupitirizabe Kuwononga ku California

Moto wolusa ukuwononga kwambiri ku California, U.S.A. Moto umene wawononga kwambiri ndi umene akuutchula kuti Dixie Fire womwe wawononga malo aakulu kwambiri oposa maekala 463,476. Panopa, motowu uli pa nambala 2 pa moto onse umene wakhala ukuwononga ku California.

Mmene Motowu Wakhudzira Abale ndi Alongo Athu

  • ofalitsa okwana 415 achoka m’nyumba zawo

  • nyumba zokwana 17 zawonongeka

  • nyumba ziwiri zawonongeka kwadzaoneni

Ntchito Yothandiza Anthu

  • Oyang’anira madera a m’madera amene akhudzidwa ndi motowu, akumalumikizana ndi akulu m’mipingo pofuna kuwonetsetsa kuti abale ndi alongo amene akhudzidwa akulimbikitsidwa mwauzimu komanso kuti akulandira thandizo limene akufunikira. Akuonetsetsanso kuti amene athawa m’nyumba zawo awapezera malo okhala oti abayembekezerako.

  • Onse amene akugwira ntchito yothandiza anthuyi akuyesetsa kutsatira malangizo onse opewera COVID-19

Ngakhale pa nthawi imene tikukumana ndi mavuto, anthu a Yehova amayesetsa kukhala mabwenzi enieni, okonzeka kuthandiza abale ndi alongo awo.—Miyambo 17:17.