Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

SEPTEMBER 1, 2020
UNITED STATES

Moto Wolusa Wasakaza Chakumadzulo kwa United States

Moto Wolusa Wasakaza Chakumadzulo kwa United States

Malo

Kumpoto kwa California ndi ku Oregon

Ngozi yake

  • Kunagwa ziphaliwali zosachepera 14,000 ndipo zimenezi komanso zinthu zina zinayambitsa moto wolusa womwe unayaka maulendo oposa 700 n’kuwononga dera loposa maekala 1 miliyoni kumpoto kwa California ndi m’madera ena ku Oregon

  • Mpweya wawonongeka kwambiri chifukwa cha utsi ndi phulusa. Lipoti lomwe linatuluka pa 21 August linanena kuti patsikuli kumpoto kwa California kunali mpweya woipa kwambiri kuposa dera lina lililonse padzikoli

  • Magulu awiri a moto womwe ukuyakabe panopa akuoneka kuti ali m’gulu la magulu atatu a moto wolusa kwambiri womwe wakhala ukuyaka m’mbuyomu ku California

Mmene motowu wakhudzira abale ndi alongo athu

  • Ofalitsa 936 anafunika kuchoka kaye m’nyumba zawo

Katundu amene wawonongeka

  • Nyumba ziwiri za ofalitsa zapsa

Ntchito yothandiza anthu

  • Komiti Yothandiza pa Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi, oyang’anira madera komanso akulu am’mipingo akugwirira ntchito limodzi pothandiza abale ndi alongo amene akhudzidwa

Abale ndi alongo athuwa akuyamikira kwambiri abale padziko lonse chifukwa chowathandiza. M’bale wina anati: “Vuto lililonse limene lingatigwere, abale ndi alongo athu amathandiza nthawi yomweyo. Ndifedi banja limodzi.” Ntchito yothandiza abale athu omwe akhudzidwa ikupitirira ndipo umenewu ndi umboni wakuti palibe chimene chingathe “kutilekanitsa ndi chikondi cha Mulungu.”—Aroma 8:39.