Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

NOVEMBER 20, 2019
UNITED STATES

Moto Wolusa Wawononga Kwambiri M’madera Ena ku California

Moto Wolusa Wawononga Kwambiri M’madera Ena ku California

M’miyezi yaposachedwapa, moto wolusa unayaka ku California ndipo unawotcha dera lokwana makilomita 362 m’mbali zake zonse ndipo unawononga mbali yaikulu kwambiri ya derali.

Ofesi ya nthambi ya United States yanena kuti abale ndi alongo oposa 1,700 anathawa chifukwa motowu unafika mbali zosiyanasiyana. Palibe yemwe anavulala kapena kufa. Moto wodziwika ndi dzina loti Sandalwood Fire unayamba pa 10 October, 2019, mumzinda wa Calimesa ndipo unawononga nyumba ya m’bale wathu wina. Nyumba zinanso zinawonongeka chifukwa cha utsi. Pofika pano pafupifupi anthu onse omwe anathawa abwerera m’nyumba zawo.

Mkulu wina yemwe amakhala m’dera lina lomwe linakhudzidwa ndi motowu anati, “Taona kuti kumvera malangizo n’kofunika kwambiri zoterezi zikachitika. Motowu utangoyamba, abale amene anali m’madera angozi kwambiri anathawa nthawi yomweyo ndipo zimenezi zinathandiza kuti ozimitsa moto angogwira ntchito yozimitsa moto m’malo molimbana ndi kufufuza anthu.”

Oyang’anira madera ndi akulu akupitiriza kuyendetsa ntchito yopereka chithandizo kwa anthu omwe anathawa m’nyumba zawo chifukwa cha motowu. N’zolimbikitsa kwambiri kuona chikondi komanso mzimu wochereza womwe ofalitsa a m’maderawa akusonyeza. Ponena za chikondi chimene Akhristu amasonyezana, woyang’anira dera wina anati, “Sitinavutike kupeza nyumba zoti anthu onse omwe anathawa azikhalamo.”

Tikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa cha onse omwe ‘athandiza ndi kulimbikitsa’ abale ndi alongo athu omwe akhudzidwa ndi moto wolusawu.—Akolose 4:11.