Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

OCTOBER 19, 2020
UNITED STATES

Mphepo Yamkuntho (Hurricane Delta) Yasakaza ku Louisiana

Mphepo Yamkuntho (Hurricane Delta) Yasakaza ku Louisiana

Malo

Ku Louisiana komanso kum’mwera chakum’mawa kwa Texas

Ngozi yake

  • Pa 9 October 2020, mphepo yamkuntho yamphamvu kwambiri inawomba ku Louisiana ndipo inaononganso zinthu m’madera amene anakhudzidwa ndi mphepo ina yamkuntho yotchedwa Laura posachedwapa

  • Mphepoyi inali yosakanikirana ndi mvula yamphamvu kwambiri zomwe zinachititsa kuti madzi asefukire komanso magetsi azime m’madera ambiri

Mmene mphepoyi yakhudzira abale ndi alongo athu

  • Ofalitsa 1,583 anasamutsidwa kapenanso kuthawa m’nyumba zawo

Katundu amene wawonongeka

  • Nyumba 216 ndi Nyumba za Ufumu 16 zawonongeka pang’ono

  • Nyumba 7 zawonongeka kwambiri

  • Nyumba zitatu zagweratu

Ntchito yothandiza anthu

  • Oyang’anira madera ndi akulu a mipingo akuthandiza abale ndi alongo amene akufunikira chakudya, madzi, pokhala ndi zinthu zina. Abalewa akugwira ntchitoyi mogwirizana ndi Makomiti Othandiza pa Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi amene anathandiza anthu pa nthawi ya Mphepo Yamkuntho ya Laura. Abale athuwa akuyesetsa kuchita zinthu mosamala potsatira malangizo opewera mliri wa COVID-19

Nawonso akulu a mipingo akuyesetsa kuchita khama polimbikitsa abale omwe akhudzidwa pogwiritsa ntchito mfundo za m’Malemba. Mkulu wina ananena kuti: “N’zolimbikitsa kwambiri kuona kuti Yehova wakhala akupatsa mphamvu abale ndi alongo amenewa. Iye akuwapatsadi ‘mphamvu zoposa zachibadwa.’”—2 Akorinto 4:7.

Tikuthokoza Yehova chifukwa akupitiriza kukhala “pothawirapo ndi pobisalirapo” pa abale ndi alongo athu okondedwa omwe akhudzidwa ndi mphepo zamkuntho zomwe zachitika posachedwapa.—Yesaya 4:6.