Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

AUGUST 14, 2020
UNITED STATES

Mphepo Yamkuntho (Hurricane Isaias) Yawononga Zinthu Kum’mawa kwa United States

Mphepo Yamkuntho (Hurricane Isaias) Yawononga Zinthu Kum’mawa kwa United States

Malo

Kum’mawa kwa United States

Ngozi

  • Mphepo yamkuntho (Hurricane Isaias) inawononga zinthu ku North Carolina pa 3 August 2020

  • Mphepoyi inkawononga zinthu zambirimbiri ikulowera kunyanja chakum’mawa moti magetsi anazima

Mmene yakhudzira abale ndi alongo

  • Mlongo mmodzi wavulala

  • Mabanja 12 asamuka

Zinthu zimene zawonongeka

  • Nyumba 55 za abale zawonongeka pang’ono

  • Nyumba 5 zawonongeka kwambiri

  • Magalimoto ambiri anawonongedwa

  • Nyumba za Ufumu 5 zawonongeka pang’ono

Zimene zachitika powathandiza

  • Oyang’anira madera ndi akulu m’mipingo anagwira ntchito yothandiza abale ndi alongo amene akhudzidwa ndi ngoziyi ndipo ankachita izi motsatira njira zopewera COVID-19

Tikuyamikira kuti Yehova akuthandiza abale ndi alongo amene akhudzidwa ndi mphepoyi. Tikungoyembekezera nthawi imene aliyense sadzaopa tsoka lobwera chifukwa cha ngozi zochitika m’chilengedwe.—Miyambo 1:33.