Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Magalimoto anangosiyidwa mumsewu waukulu wa Interstate 45 ku Houston, Texas

OCTOBER 2, 2019
UNITED STATES

Mphepo Yamkuntho Yachititsa Kuti Madzi Asefukire Kwambiri Kum’mwera Chakum’mawa kwa Texas

Mphepo Yamkuntho Yachititsa Kuti Madzi Asefukire Kwambiri Kum’mwera Chakum’mawa kwa Texas

Mlungu woyambira pa 16 September, 2019, mphepo yamkuntho ya Imelda inawononga kum’mwera chakum’mawa kwa Texas. Mphepoyi inachititsa kuti kugwe mvula yambiri (masentimita oposa 102) kwa masiku ochepa okha. Akatswiri ena akukhulupirira kuti mphepo ya Imelda ndi imodzi mwa mphepo zamkuntho zomwe zinagwetsa mvula yambiri m’dziko la United States. Mphepoyi itawomba, magalimoto ambirimbiri anangosiyidwa m’misewu ikuluikulu ndi m’misewu ina. Anthu ambiri anasamutsidwa m’nyumba zawo.

Malipoti oyambirira ochokera ku ofesi ya nthambi ya United States akusonyeza kuti palibe wa Mboni aliyense yemwe anavulala kapena kufa. M’madera omwe anakhudzidwa ndi mphepoyi muli a Mboni 29,649. Komabe, ofalitsa 114 anathawa m’nyumba zawo. Kuwonjezera pamenepa, nyumba 145 za abale athu komanso Nyumba za Ufumu 10 zinawonongeka.

Komiti Yothandiza Pangozi Zogwa Mwadzidzidzi yasankhidwa ndi ofesi ya nthambi ndipo ikugwira ntchito limodzi ndi oyang’anira madera ndi akulu kuti aone zinthu zomwe zaonongeka komanso kupereka chithandizo. Tikudziwa kuti Yehova athandiza abale athuwa popeza kuti ‘kukoma mtima kwake kosatha kumafika kumwamba.’—Salimo 36:5.