Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

6 AUGUST, 2020
UNITED STATES

Mphepo Yamkuntho Yotchedwa Hurricane Hanna Inawomba ku Texas

Mphepo Yamkuntho Yotchedwa Hurricane Hanna Inawomba ku Texas

Malo

Texas, United States

Ngozi yake

  • Mphepo yoopsa kwambiri yotchedwa Hurricane Hanna inafika m’mbali mwa nyanja m’chigawo cha Texas pa 25 July 2020. Zimenezi zinachititsa kuti madzi asefukire komanso kuti nyanja ikwere kwambiri

  • Mphepo yamkunthoyi ndi yoyamba kuwomba panyanja ya Atlantic chaka chino

Mmene mphepoyi yakhudzira abale ndi alongo athu

  • Abale awiri anavulala, koma osati modetsa nkhawa

  • Ofalitsa 193 ankafunika kuchoka m’nyumba zawo kwa kanthawi

Nyumba zomwe zinawonongeka

  • Nyumba 347 za abale zinawonongeka pang’ono

  • Nyumba 31 zinawonongeka kwambiri

Ntchito yothandiza anthu

  • Oyang’anira dera limodzi ndi akulu, akumalimbikitsa komanso kuthandiza abale ndi alongo am’mipingo ya m’chigawo chomwe chinakhudzidwa ndi ngoziyi

Ndife osangalala kuti Yehova, yemwe ndi “Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse,” akupitiriza kusamalira abale ndi alongo athu a ku Texas pa nthawi yovutayi.​—2 Akorinto 1:3, 4.