7 SEPTEMBER, 2020
UNITED STATES
Mphepo Yamkuntho Yotchedwa Hurricane Laura Yawononga ku Louisiana
Malo
Arkansas, Mississippi, kumadzulo kwa Louisiana ndi kum’mawa kwa Texas
Ngozi yake
Chimphepo champhamvu chinasakaza zinthu kumadzulo kwa Louisiana pa 27 August 2020 ndipo magetsi anazima
Mmene yakhudzira abale ndi alongo
N’zomvetsa chisoni kuti mlongo wina wachikulire anamwalira pamene ankasamutsidwa kumalo amene ankalandira chithandizo chakuchipatala
Mlongo wina anavulala pang’ono
Ofalitsa 3,992 anasamutsidwa kunyumba zawo
Zinthu zimene zawonongeka
Nyumba 10 za abale zawonongekeratu
Nyumba 95 ndi Nyumba za Ufumu 4 zawonongeka kwambiri
Nyumba 192 ndi Nyumba za Ufumu 16 zawonongeka pang’ono
Kuthandiza amene akhudzidwa
Nthambi ya ku United States yakhazikitsa komiti yoti ithandize pa ngozi imeneyi
Oyang’anira madera ndi akulu m’mipingo akuthandiza ofalitsa amene asamutsidwa kuti apeze malo okhala
Zimene zachitika
Abale a m’madera apafupi analola kuti akhristu anzawo adzafikire m’nyumba zawo koma ankayesetsa kuchita zonse zothandiza popewa COVID-19. M’bale wina amene anasamutsidwa anati: “Zonsezi ndi umboni wakuti Yehova akutidalitsa!”
Abale ndi alongo amene ayesetsa kutsatira malangizo komanso kuthandiza anzawo amene akhudzidwa ‘asonyeza kuti iwowo ndi atumiki a Mulungu’ enieni.—2 Akorinto 6:4.