Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kumanzere: Mphepo yamkuntho ya Helene ikuwomba cha ku Mexico pa 26 September 2024. M’mwamba kumanja: Madzi asefukira pa Nyumba ya Ufumu ku Swannanoa, ku North Carolina, U.S.A. M’munsi kumanja: Mitengo yagwera pa nyumba ya m’bale ku Asheville, ku North Carolina

3 OCTOBER 2024
UNITED STATES

Mphepo Yamkuntho ya Helene Yawononga Kwambiri Kum’mwera Chakum’mawa kwa United States

Mphepo Yamkuntho ya Helene Yawononga Kwambiri Kum’mwera Chakum’mawa kwa United States

Pa 26 September 2024, mphepo yamphamvu kwambiri ya Helene inafika m’madera a m’mbali mwa nyanja ku Florida, U.S.A. Mphepo yoopsayi inachititsa kuti kugwe mvula yambiri komanso mphepo inkathamanga pa liwiro la makilomita 225 pa ola limodzi. Pa 27 September, mphepo yowononga ya Helene inafika kumtunda. Pa nthawiyi mphepoyi inkathamanga pa liwiro la makilomita 95 pa ola limodzi kulowera ku Georgia. Tsiku lotsatira, mphepoyi inapitiriza kulowera chakumpoto, ku South Carolina ndipo inachititsa kuti kuwombe mphepo zina zitatu zamkuntho. Pamene mphepo ya Helene inafika ku North Carolina, m’mizinda yambiri munagwa mvula yoposa masentimita 90.

Mphepoyi yomwe inabweretsa mvula yamphamvu inachititsa kuti madzi asefukire n’kuwononga nyumba zambiri, malo ochitira malonda komanso misewu. Mpaka pano, anthu oposa 1 miliyoni akukhalabe opanda magetsi. Anthu pafupifupi 180 anafa.

Mmene Mphepoyi Yakhudzira Abale ndi Alongo Athu

  • N’zomvetsa chisoni kuti abale athu atatu anafa

  • Ofalitsa 7 anavulala pang’ono

  • Ofalitsa 1,606 akusowa pokhala

  • Nyumba 29 zinagweratu

  • Nyumba 236 zinawonongeka kwambiri

  • Nyumba 779 zinawonongeka pang’ono

  • Nyumba ya Ufumu imodzi inawonongeka kwambiri

  • Nyumba za Ufumu 19 zinawonongeka pang’ono

Ntchito Yopereka Chithandizo

  • Oyang’anira madera komanso akulu akulimbikitsa anthu amene akhudzidwa pogwiritsa ntchito Baibulo komanso kuwathandiza m’njira zina

  • Pakhazikitsidwa Makomiti Othandiza Pakachitika Ngozi Zamwadzidzidzi awiri kuti atsogolere ntchito yothandiza anthu

Tili ndi chisoni chifukwa cha anthu amene afa ndi mphepo yoopsayi. Komabe tikulimbikitsidwa tikaganizira za lonjezo la Yehova lakuti m’tsogolo anthu onse “adzakhala motetezeka ndipo sadzasokonezeka chifukwa choopa tsoka.”​—Miyambo 1:33.