17 OCTOBER 2024
UNITED STATES
Mphepo Yamkuntho ya Milton Yawononga ku Florida, U.S.A.
Pa 9 October 2024, mphepo yamkuntho ya Milton inafika m’madera a m’mbali mwanyanja ku Florida, U.S.A., ndipo inawononga kwambiri. Mphepo yamphamvuyi inawomba pasanathe mawiki awiri kuchokera pamene mphepo yamkuntho ya Helene inawombanso m’dera lomweli zomwe zinachititsa kuti madzi asefukire kwambiri n’kuwononga zinthu. Mphepo ya Milton inkathamanga pa liwiro la makilomita 289 pa ola limodzi. M’madera ambiri a m’mbali mwanyanja munagwa mvula yochuluka masentimita 45 komanso panyanja pankawomba mafunde aatali mamita atatu zomwe zinachititsa kuti madzi asefukire kwambiri.
Kuwonjezera pamenepo, mphepo ya Milton inachititsanso mphepo zina zokwana 38 m’zigawo za kum’mwera ndi pakati pa Florida zomwe zinachititsa kuti zinthu zambiri ziwonongeke. Anthu pafupifupi 80,000 akukhalabe opanda magetsi ndipo anthu pafupifupi 24 anafa.
Mmene Mphepoyi Yakhudzira Abale ndi Alongo Athu
Palibe m’bale kapena mlongo amene wafa
Ofalitsa awiri anavulala kwambiri
Ofalitsa 4 anavulala pang’ono
Ofalitsa 9,949 achoka m’nyumba zawo kapena akusowa pokhala
Nyumba 16 zinagweratu
Nyumba 235 zinawonongeka kwambiri
Nyumba 1,398 zinawonongeka pang’ono
Nyumba ya Ufumu imodzi inawonongeka pang’ono
Nyumba za Ufumu 30 zilibe magetsi pakadali pano ndipo sizingagwiritsidwe ntchito
Ntchito Yopereka Chithandizo
Kutatsala masiku awiri kuti mphepo ya Milton iwombe, ofesi ya nthambi ya United States inatumiza kalata ku mipingo yoposa 800 yomwe ili m’dera limene mphepoyi inkayembekezereka kuti ifika. Kalatayi inali ndi malangizo othandiza kwa amene akanafuna kusamuka m’nyumba zawo
Oyang’anira madera komanso akulu akulimbikitsa anthu amene akhudzidwa pogwiritsa ntchito Baibulo komanso kuwathandiza m’njira zina
Pakhazikitsidwa Makomiti Othandiza Pakachitika Ngozi Zamwadzidzidzi atatu kuti atsogolere ntchito yothandiza anthu omwe akhudzidwa ndi mphepo ya Milton komanso Helene
A Mboni za Yehova ambiri a ku Georgia ndi ku South Carolina, ku U.S.A., analandira mwachikondi abale ndi alongo awo amene analibe pokhala
Tonse mogwirizana monga abale ndi alongo, tikupempha Yehova kuti apitirize kukhala “malo othawirapo komanso achitetezo” kwa anthu onse amene akhudzidwa ndi mphepo zamkunthozi.—Yesaya 4:6.