Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

SEPTEMBER 24, 2020
UNITED STATES

Mphepo Yamkuntho ya Sally Yavuta ku United States

Mphepo Yamkuntho ya Sally Yavuta ku United States

Malo

Alabama, Florida ndi Mississippi

Ngozi yake

  • Pa 16 September 2020, chimvula chophatikizana ndi mphepo yamkuntho chinagwa ku Alabama ndipo chinachititsa kuti madzi asefukire m’kanthawi kochepa

  • Mphepo yamkunthoyi inawononga zinthu zambiri komanso m’madera ambiri magetsi anazima

Mmene mphepoyi yakhudzira abale ndi alongo athu

  • Ofalitsa 240 anasamuka m’nyumba zawo

  • Wofalitsa mmodzi anavulala pang’ono

Katundu amene wawonongeka

  • Nyumba 143 za anthu ndi Nyumba za Ufumu 11 zawonongeka pang’ono

  • Nyumba 12 za anthu ndi Nyumba ya Ufumu imodzi zawonongeka kwambiri

Ntchito yothandiza anthu

  • Makomiti awiri othandiza pa ngozi zogwa mwadzidzidzi akugwira ntchito limodzi ndi oyang’anira madera komanso akulu a m’mipingo kuti asamalire abale ndi alongo amene ali m’madera okhudzidwa, powalimbikitsa mwauzimu komanso kuwapatsa zinthu zimene akufunikira. Iwo akuchita zimenezi kwinaku akuyesetsa kutsatira malangizo opewera matenda a COVID-19

Wofalitsa wina ananena kuti anali ndi nkhawa kwambiri chimvulachi chitangogwa kumene. Koma atathandizidwa ndi abale ndi alongo a mumpingo wakwawo, iye anayamikira kwambiri ndipo anati: “Panopa ndikuchita kusowa chonena ndikaona mmene abale ndi alongo andithandizira komanso kundisonyeza chikondi.”—1 Yohane 3:18.