Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Magalimoto ali m’madzi omwe anasefukira mumsewu wolowera kunyumba ya banja lina la Mboni mumzinda wa Harlingen ku Texas

JULY 10, 2019
UNITED STATES

Mphepo Yamphamvu Komanso Madzi Osefukira Zaononga Kum’mwera kwa Texas

Mphepo Yamphamvu Komanso Madzi Osefukira Zaononga Kum’mwera kwa Texas

Pa 24 June, 2019, mphepo yamphamvu komanso mvula yamphamvu zinaononga kum’mwera kwa Texas. Malipoti akusonyeza kuti madzi osefukira anawononga nyumba zambiri ndipo anthu oposa 100 anasamutsidwa m’nyumba zawo.

Ngakhale kuti palibe ofalitsa aliyense amene anavulala ndi mphepoyo, ofalitsa 47 anathawa m’nyumba zawo. Kuonjezera pamenepo, mphepoyo inaononga nyumba 65 za abale ndi alongo athu komanso nyumba imodzi imene inamangidwa molumikizidwa ku Nyumba ya Ufumu.

Oyang’anira madera komanso akulu akuchita maulendo aubusa kwa amene anakhudzidwa ndi mphepo yamkunthoyo. Komanso Komiti Yothandiza Pangozi Zadzidzidzi ikuyendetsa ntchito yowapezera pokhala, kugawa chakudya, madzi, komanso zovala. Abale ayamba kale kugwira ntchito yoyeretsa komanso yokonza nyumba zomwe zinaonongeka ndiponso nyumba yomwe inamangidwa pa Nyumba ya Ufumu.

Tipitirizabe kuthandiza abale ndi alongo athu kum’mwera kwa Texas pamene akudalira Yehova komanso kupirira mavuto omwe abwera chifukwa cha nyengo yovuta kwambiri imeneyi.—Yesaya 26:3, 4.