Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MARCH 14, 2019
UNITED STATES

Mphepo Zamkuntho Zapha Anthu Kum’mwera Chakum’mawa kwa United States

Mphepo Zamkuntho Zapha Anthu Kum’mwera Chakum’mawa kwa United States

Lamlungu pa 3, March 2019, mphepo zamkuntho zinaomba m’madera ena ku Alabama, Florida, ndi ku Georgia. Anthu 23 anafa ndipo enanso ambiri anavulala chifukwa cha mphepozi.

Lipoti lochokera ku ofesi ya nthambi ya ku United States likusonyeza kuti palibe wa Mboni aliyense yemwe wafa. Komabe, mlongo wathu wina anavulala mphepo yamkuntho itawonongeratu nyumba yake mumzinda wa Fort Valley ku Georgia. Panopa mlongoyu akulandira thandizo la mankhwala pachipatala china chapafupi. Kuwonjezera pamenepo, ofesi ya nthambi yanena kuti nyumba 6 za abale zinawonongeka ndipo zinanso 4 zinawonongekeratu. Mogwirizana ndi malangizo ochokera kwa oyang’anira madera, ofalitsa anapereka zakudya, malo okhala komanso zovala kwa abale ndi alongo omwe anakhudzidwa ndi ngozizi. Nawonso akulu a m’mipingo ya m’maderawa akulimbikitsa abale ndi alongo okhudzidwa pogwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo.

Tikupemphera kuti abale athu omwe akhudzidwa ndi ngozizi atonthozedwe ndi lemba lathu la chaka cha 2019 lomwe likuti, “Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako.”—Yesaya 41:10.