Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Mmene mphepo yamkuntho yawonongera ku Alabama

JANUARY 21, 2020
UNITED STATES

Mphepo Zamkuntho Zawononga Kum’mwera ndi Pakati ku United States

Mphepo Zamkuntho Zawononga Kum’mwera ndi Pakati ku United States

M’bale Albert Barnett ndi mkazi wake, Mlongo Susan Barnett, a mumpingo wa Tuscaloosa West, ku Alabama

Pa 11 ndi 12 January, 2020, mphepo zamkuntho zinaononga kwambiri m’madera ena a kum’mwera ndi pakati m’dziko la United States. M’madera ambiri munagwa mvula yamphamvu komanso munawomba mphepo zamkuntho zosiyanasiyana kwa masiku awiri. N’zomvetsa chisoni kuti M’bale Albert Barnett yemwe anali ndi zaka 85 ndi mkazi wake, Mlongo Susan Barnett yemwe anali ndi zaka 75, anafa mphepo yamkuntho itawononga nyumba yawo.

Ofesi ya nthambi ya United States yanenanso kuti nyumba zosachepera 4 za abale athu ndi Nyumba za Ufumu ziwiri zawonongeka pang’ono. Komanso mphepo yamkuntho inawononganso kwambiri malo amene m’bale wina amachitirapo bizinesi.

Akulu ndi woyang’anira dera akuthandiza abale ndi alongo amene akhudzidwa ndi mphepoyi powapatsa zinthu zofunikira komanso kuwalimbikitsa ndi mfundo za m’Baibulo. Tikudziwa kuti Atate wathu wakumwamba, Yehova, akutonthoza abale ndi alongo athu omwe ali ndi chisoni chifukwa cha ngoziyi.—Salimo 34:18.