23 JANUARY 2024
UNITED STATES
Munthu Womaliza pa Omaliza Maphunziro a Giliyadi M’kalasi Yoyamba Wamwalira Ali Ndi Zaka 103
Pa 23 November 2023, Mlongo Mary M. Larimer yemwe anamaliza kalasi yoyamba ya maphunziro a Watchtower Bible College of Gilead anamwalira. a Mlongo Mary anabadwa pa 4 June 1920, ku Scenery Hill, Pennsylvania, U.S.A. Iye anabatizidwa mu 1935 ali ndi zaka 15 pa msonkhano womwe unachitikira ku Washington, D.C., U.S.A. Patadutsa zaka 4, Mlongo Larimer anayamba upainiya wokhazikika ndipo amadziwika monga mlaliki wachangu.
Mu December 1942, Mlongo Larimer analandira kalata yochokera kwa M’bale Nathan Knorr, yemwe ankatsogolera ntchito za gulu lathu, kuti afunsire sukulu yomwe inkatchedwa kuti Watchtower Bible College of Gilead. Mukalatayi analembamo kuti, “Cholinga cha maphunzirowa ndi kuthandiza atumiki osankhidwa kaya akhale amuna kapena akazi, kuti agwire ntchito ya umishonale kulikonse padzikoli.” Analembanso kuti: “Maphunzirowa azichitika kwa miyezi 5 . . . Mudzafunika kuphunzira mwa khama kwambiri kuti mudzamalize maphunzirowa pa miyezi yochepayi.” Nthawi yomweyo mlongoyu anatumiza mafomu ake ofunsira sukuluyi.
Pa 1 February 1943, mlongoyu limodzi ndi ophunzira ena 99 anayamba maphunziro awo a sukuluyi yomwe inali ku South Lansing, New York, U.S.A. Pa miyezi yonse 5 imene ankachita maphunzirowa, Mlongo Mary ankawerenga mwakhama kwambiri kuti adziwe malemba molondola. Analidi wophunzira wakhama kwambiri ndipo anamaliza maphunzirowa pa 23 June 1943.
Atamaliza maphunzirowa, Mlongo Mary atumizidwa ku Cuba monga mmishonale. Pofotokoza ena mwa mavuto omwe ankakumana nawo pa utumiki wakewu, mlongoyu ananena kuti: “Anthu anali osauka. Tinkafunika kuyenda popita muutumiki . . . Tinalibe galimoto.” Mlongo Mary anakhalabe ku Cuba mpaka mu 1948 pamene anabwerera ku Pennsylvania kuti akasamalire mayi awo omwe anavulala kwambiri. Mlongo Mary anakhalabe wosakwatiwa ndipo ankatumikira Yehova mwakhama kwambiri. Iye wamwalira akutumikirabe Yehova mumpingo wa Glendale, ku California, U.S.A.
Panopa, Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo ili ku Patterson, New York ndipo panopa ikuphunzitsa ophunzira a kalasi nambala 155. M’bale Mark Noumair, yemwe ndi mlangizi wa sukulu ya Giliyadi atamva za imfa ya Mlongo Mary ananena kuti: “Mlongo Mary Larimer anali kamtsikana kochokera mu tauni yaing’ono koma anali wofunitsitsa kupita kumadera achilendo kuti akauze anthu zokhudza Yehova. Sankadziwa kuti atumizidwa kuti komanso ngati angakabwereko n’komwe. Amishonale omwe anamaliza maphunziro a Giliyadi ngati Mlongo Mary anathandiza kwambiri pa ntchito yolalikira, zomwe zachititsa kuti padziko lonse pakhale ofalitsa ambiri.”—Yesaya 6:8
a Mu 1946, dzina lakuti Watchtower Bible College of Gilead linasinthidwa kukhala Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo.