JUNE 13, 2019
UNITED STATES
Mvula Ndi Mphepo Zamphamvu Kwambiri Zaononga Madera Ena ku United States
Malipoti akusonyeza kuti m’mwezi wa May 2019, mvula yamphamvu komanso mphepo zamkuntho zokwana 500 zinaononga ku United States.
A Mboni za Yehova ku Arkansas, Indiana, Mississippi, Missouri, Ohio, Oklahoma, Pennsylvania, ndi ku Texas anakhudzidwa ndi nyengo yoopsayi. Palibe m’bale kapena mlongo aliyense amene anafa. Komabe, a Mboni okwana 6 anavulala ndipo 4 mwa amenewa anagonekedwa m’chipatala. Kuwonjezera pamenepa, nyumba 6 za abale athu zinagweratu ndipo nyumba 98 komanso Nyumba za Ufumu 12 zinaonongeka. Zimenezi zinachititsa kuti abale ndi alongo athu 84 athawe m’nyumba zawo.
Abale akupitiriza kufufuza zinthu zomwe zinaonongeka ndipo akupereka chakudya, madzi komanso malo okhala kwa amene anakhudzidwa. Akulu ndi oyang’anira madera akutonthoza komanso kulimbikitsa abale okhudzidwa pogwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo.
Tipitiriza kuthandiza ndiponso kupempherera abale athuwa pamene akupirira mavuto obwera chifukwa cha mphepozi.—2 Akorinto 1:3, 4.