Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JULY 22, 2019
UNITED STATES

Mvula Yamkuntho ya Barry Yawononga Nyumba Zambiri Kum’mwera kwa United States

Mvula Yamkuntho ya Barry Yawononga Nyumba Zambiri Kum’mwera kwa United States

Loweruka pa 13 July, 2019, mphepo yamphamvu inaomba ku Louisiana koma inachepa mphamvu mwamsanga n’kukhala mvula yamkuntho yotchedwa Barry. Mvula yamkunthoyi inachititsa kuti nyumba zionongeke, madzi asefukire, komanso kuti magetsi azime ku Alabama, Louisiana, ndi Mississippi.

Ngakhale kuti palibe wofalitsa aliyense amene anavulala kapena kuphedwa ndi mvula yamkunthoyi, ofalitsa 123 anathawa m’nyumba zawo. Mvula yamkunthoyi inaononganso nyumba 27 za abale ndi alongo athu ndiponso Nyumba za Ufumu 5.

Oyang’anira madera komanso akulu a m’maderawa akulimbikitsa abale ndi alongo omwe akhudzidwa ndi mvula yamkunthoyi. Komanso ofalitsa a mipingo yapafupi akupereka madzi, chakudya, ndiponso malo ogona kwa amene akufunika zinthuzi. Abale a m’maderawa ayamba kale kukonzekera kugwira ntchito yokonza zinthu zomwe zinaonongeka.

Tipitiriza kupempherera komanso kuthandiza abale ndi alongo athu amene akhudzidwa ndi mvula yamkuntho ya Barry kum’mwera kwa United States.—Miyambo 18:10.