Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

AUGUST 20, 2020
UNITED STATES

Mvula ya Ziphaliwali Yawononga Kwambiri ku United States

Mvula ya Ziphaliwali Yawononga Kwambiri ku United States

Malo

Pakati chakumadzulo kwa United States

Ngozi yake

  • Pa 10 August 2020, m’madera ena a m’dzikoli munagwa mvula ya ziphaliwali ndiponso munawomba mphepo yamphamvu yomwe inawononga zinthu zambiri

  • Mphepoyi inawononga mbewu ndi katundu ndipo magetsi anazima m’madera ambiri

Mmene mvulayi yakhudzira abale ndi alongo athu

  • Ofalitsa awiri anavulala pang’ono

  • Ofalitsa 18 anachoka m’nyumba zawo

Katundu amene wawonongeka

  • Nyumba 216 zinawonongeka pang’ono

  • Nyumba 5 zinawonongekeratu

  • Nyumba za Ufumu 24 zinawonongeka pang’ono

Ntchito yothandiza anthu

  • Makomiti Othandiza pa Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi akupitirizabe kugwira ntchito limodzi ndi oyang’anira madera komanso akulu am’mipingo pothandiza abale ndi alongo amene akhudzidwa ndi ngoziyi

Pamene Yehova akupitiriza kuthandiza abale ndi alongo omwe ali m’maderawa, tikuyembekezera mwachidwi nthawi imene anthu sadzasowanso pokhala chifukwa cha ngozi zam’chilengedwe.—Yesaya 65:21.